Upload
others
View
0
Download
0
Embed Size (px)
Citation preview
KAPANGIDWE NDI KAGWIRITSIDWE NTCHITO KA
KOMPOSITI NDI FETELEZA
MANURE, COMPOST AND FERTILIZER MANAGEMENT
MAU OYAMBA
Chipalamba chimachitika ngati zinthu monga kusamalira ndi kudzala mitengo, kulima
mwakasinthasintha komanso mwadongosolo ndi zina zomwe zimapangitsa kuti nthaka ikhale
yachonde sizikutsatidwa. Zotsatira zake ndi zakuti zokolola pa munda zimakhala zochepa
poyerekeza ndi zomwe tikanakolola nthaka ili bwino bwino.
Zinanso zomwe zapangitsa kuti nthaka iguge ndi kudzala mothinana, kugwiritsa ntchito fetereza
mopsyola muyeso, kulima mosatsatira njira zotetezera nthaka.
Kupanga ndi kugwiritsa ntchito kompositi ndi njira yokhayo yomwe tiyenera kulimbikitsana.
Kabukuka kalembedwa ndicholinga chakuti tikumbutsane kufunikira kwa kupanga komanso
kugwiritsa ntchito Kompositi.
Ambiri amakhulupilira kugwiritsa ntchito ndowe za ziweto ngati manyowa. kudalira ndowe zokha
sikokwanira chifukwa ziweto sizokwanira komanso sizikhala malo amodzi kuti zipange ndowe
zambiri.
1
MITUNDU YA FETELEZA
Feteleza ndi mchere umene umapezeka munthaka ngati chakudya cha mbewu kuti zikule ndi
kubeleka bwino. Pali feteleza wopangidwa mu njira ya chilengedwe yemwe zitsanzo zake ndi
manyowa komanso ndowe pongotchulapo zina komanso feteleza wopangidwa mu njira za
sayansi. Feteleza uyu ndi yemwe anthu ambiri tikumudziwa monga UREA, DAP pongotchulapo
wina wochepa.
Feteleza opangidwa m’njira ya sayansi
Pali feteleza okhala ndi chakudya cha m’tundu umodzi ndi wina okhala ndi zakudya zingapo za
mbeu.
Feteleza wa chakudya cha mtundu umodzi:
Fetelezayu amakhala ndi chimodzi mwa zakudya za mbeu izi nitrogen, phosphate kapena
potassium (Urea, Superphosphate, Potassium Chloride)
Feteleza okhala ndi zakudya zingapo zambeu:
Fetelezayu amakhala ndi ziwiri kapena zingapo mwa zakudya za mbeu izi nitrogen, phosphate
kapena potassium zonse mu kam’bulu kamodzi ka feteleza.
Kumasulira manambala a pa nthumba la feteleza
Nambala ili yonse ikusonyeza kuchuluka kwa zakudya mwa ndondomeko
iyi: nitrogen, phosphate ndi potassium kuchoka kumanzere kupita
kumanja. Thumba ili likusonyeza kuti kuchuluka kwa n’tundu uliwonse pa
100gramms ndi kofanana (14% wina aliyense).
Ubwino ndi kuipa kogwiritsa ntchito fetereza:
Ubwino - Amakhala ndi zakudya zingapo za
mbeu
- Ndi osabvuta kuthira
-amapeleka zakudya za mbeu
pompopompo
-sachedwa kusungunuka
Kuipa - Ndiowopsya ku nthupi la
munthu
- Ndiwodula (okwera mtengo)
- Akhonza kuwononga madzi ndi
chilengedwe china
- Amagugitsa nthaka
- Sachedwa kutsukika ndi mvula
- Sabwezeretsa chonde
- atha kuwawula mbeu ngati
sitinatsate dongosolo la
kathiridwe
2
Table 1. Mawonekedwe ena afeteleza wokhala ndi chakudwa chimodzi
Feteleza Zomwe
zilimo Mawonekedwe ake
Sulphate of ammonia
(Washuga)
21% N
� Wosungunuka mmadzi
� Amapangisa nthaka kukhala ya
nchere
� Sapita pansi nsanga
� Sayamwa chinyezi kuchokera kunja
� Zotsalira zake zimawoneka ngati
zoyera ndipo ali ngati suga
Urea 46% N
� Amasungunuka mmadzi nsanga
� Sapereka mchere ku nthaka
� Amagwira ntchito nsanga
� Amayamwa chinyontho kunja
� Amawoneka woyera
CAN 26-28% N +
Calcium
� Amasungunuka mmadzi nsanga
� Amathandiza kuchepesa mchere wa
munthaka ngati wachuluka
� Amayamwa chinyontho kunja
� Amasamalira nthaka ndi
kubwezeretsedwa ngati ku
chilengedwe.
� Amawoneka ngati wa chikasu kapena
woyelerako pang’ono
Single Super phosphate 8.5% P2O5
� Amasungunuka mmadzi nsanga
� Samasungunuka munthaka yomwe ili
ndi mchere
� Amawoneka ngati wa chikasu kapena
woyelerako pang’ono
Double Super phosphate 45% P2O5
� Amasungunuka mmadzi nsanga
� Samasungunuka munthaka yomwe ili
ndi mchere
� Sapereka mchere ku nthaka
� Zotsalira zimawoneka ngati za mbuu
pang’ono
Sulphate of Potash 40% K2O
� Amasungunuka nsanga
� Sapita pansi nsanga
� Amawoneka ngati wosefeka komanso
wa chikasu.
Muriate of Potash 60% K2O � Amasungunuka nsanga
� Sapita pansi nsanga
3
FETELEZA WACHILENGEDWE
Manyowa ochokera m’khola la ziweto
Awa ndi manyowa opangidwa kuchokera ku ndowe ndi mkodzo wa ziweto. Ziwetozi ndi monga
ng’ombe, mbuzi, nkhosa, nkhumba komanso nkhuku ndi zina. Manyowawa amakhala ndi
mphamvu yochulukirapo yobiliwiritsa (nitrogen N) ndi kulimbitsa (potassium K) Koma
amafooka pakhani yokhwimitsa mbewu (phosphorus P). Ubwino/mphamvu za manyowawa
zimadalira zaka ndi mtundu wa ziweto zomwe munthu akuweta, zakudya zomwe ziwetozo
zikudya komanso kasungidwe ndi malo omwe manyowa asungidwapo.
Table 2. Zomwe mphamvu za manyowa zidalira
Zomwe manyowawa adalira Zopangidwa
Mtundu wa chiweto Ziweto monga ng’ombe zonenepetsedwera
mkhola zimapeleka manyowa amphamvu
Msinkhu wa chiweto
Nyama zazikulu zimapeleka manyowa
amphamvu komanso ochulukirapo kusiyana
ndi ana.
Mtundu wa zakudya
Kudyetsa zakudya zosiyanasiyana
kumapangitsa kuti manyowa akhale
amphamvu.
Mtundu wa zogonera � Zogonera zomwe zimayamwa
mkodzo zimawolerana mwachangu.
Kukhalitsa kwa manyowa � Manyowa okhalitsa amakhala ndi
mphamvu kusiyana ndi osakhalitsa.
Kasungidwe ka manyowa Manyowa asungidwe pa m’nthunzi osati pa
dzuwa kuopa kuti mphamvu ina ingauluke.
Kompositi
Kompositi amapangika kuchokera ku mbeu ndi nyama zomwe zawolelana kwa kanthawi.
Kuwoleranaku tikhoza kukufulumizitsa ngati tigwiritsa ntchito zinthu monga yeast kapenanso
mitundu ina ya feteteleza wa njira ya sayansi.
Kompositi ndi osabvuta kupanga ndipo amapeleka zosowekera zambiri ku mbeu zathu.
Kompositi amapangitsa kuti m’pweya ndi madzi mu nthaka zikhale zopezeka pa mulingo
wabwino ku mbeu.
Kompositi ndiwothandiza kwambiri kumunda komanso chilengedwe.
Kumunda
Kompositi amabwezeretsa chonde kuti mbeu zizikula ndi nthanzi komanso kupilira ku
matenda. Madzi ndi mpweya zimapezeka mu nthaka pa mlingo wabwino ku mbeu. Minda
imafewa polima.
Chilengedwe
Chifukwa cha kuwolerana kwa zinthu, kompositi amachepetsa kuchuluka kwa zinyalala ndipo
pakutelo kuchepetsa ndalama zomwe zingagwiritsidwe ntchito pakuchotsa zinyalalazi.
Kugwiritsa ntchito kompositi kudzakupangitsani kusiya kudalira feteleza wa njira ya sayansi
paulimi wanu ndipo pakutelo mudzachepetsa ndalama zomwe mumawononga paulimi wanu
komanso kuteteza ndi kusamala chilengedwe.
Kuti tipange kompositi wabwino pafunika zinthu zaziwisi/zobiliwila ndi zowuma. Zimenezi
zimapeleka thanzi ndi mphamvu ku tizilombo tomwe timathandiza kupanga kompositi.
4
Zinthu za ziwisi/zobiliwila ndi monga:
• Udzu oduladula
• Ndowe zaziwisi (hatchi, nkhuku, kalulu, ng’ombe)
• Zotsalira za ku kitchini (zipatso, masamba, masamba a tiyi ndi a khofi)
• Masamba awisi amitengo (green leaves)
• Zipatso zomwe zikuonongeka
Zowuma ndi monga:
• Masamba a mitengo/udzu
• Mapesi
• Zopala za matabwa
Kuti tipange kompositi pafunika:
• Zinyalala monga mapesi, masangwi, udzu, masamba a mitengo monga Gliricidia, ndiwo
za masamba zotaidwa ndi zina
• Madzi
• Phulusa
• Ndowe komanso zipangizo zina monga:
• Zikwanje
• Makasu
• Chingwe choyesera
• Ndowa
• Chifafa
• Ndodo
Table 3. Pali zinthu zina zomwe sitiyenera kugwiritsa ntchito popanga Kompositi.
0nani mu bokosi lili m’musimu
Zoyenera Zosayenera
High Nitrogen Udzu opopeledwa ndi mankhwala
Ndowe Mbeu za matenda
Zomela za m’madzi Zidutswa za zitsulo
Nkhoko Pepala la pulasitiki
Zikamba za mazira Mafuta anyama
Makoko a zipatso Ndowe za galu kapena mphaka
Masangwi
Udzu oduladula
Masese
High Carbon
Udzu wouma
Utuchi
Deya wa mpunga
Phulusa
NJIRA ZOPANGIRA MANYOWA
Pali njira ziwiri zazikulu zopangira manyowa:
5
� Njira ya pansi monga kompositi wa pa dzenje
� Njira ya pa ntunda monga Chinese, chimato, felemu ndi bokashi
Tisanayambe kupanga kompositi tiwonetsetse kuti:
• Zinyalala zonse ndi zoduladula 10-15cm
• Tasankha malo abwino opangira manyowa athu a mthunzi komanso odutsa
mpweya
• Malo achitetezo bwino
• Takumbiratu dzenje ngati tasankha mtundu umenewu
Tiyeni titsate ndondomeko izi popanga kompositi wa pa dzenje
Kumbani mayenje awiri a 2-2.5 m mulitali,
1.2-2 m mulifupi ndipo 60 cm kuzama.
Ikani zinyalala zoduladula zomwe ndi zolimba pansi ndipo
kuchuluka kwake kukhale 10cm.
Wazani madzi
-Wazani ndowe zozama 2 cm
- Ikani zinyalala zina zozama 10 cm .
- Wazani phulusa lokwana manja 10 odzadza.
- Wazani 1 cm ya dothi la pamwamba.
- Wazani madzi bwino bwino
- Pangani chimodzimodzi mpaka dzenje litadzadza ndipo lituluke
ndi 20-30cm kuchoka pa nthaka.
- Wazani mulu wanu ndi madzi.
- Phimbani ndi udzu kapena masamba a nthochi.
6
- Pisani mtengo mopingasa kuti moone ngati kompositi akuphikika. - Zulani ndodo
ndikumvetsera matethedwe.
- Ngati ndodo isakutetha pakatha masabata
awiri kapena atatu, phwasulani muluwo
ndikupanga wina mu dzenje lina.
-Yesaninso kuzika mtengo
- Kompositi wanu amakhala atapsya pakatha masabata
anayi.
KOMPOSITI WA PAMTUNDA:
Unjikani mapesi okwanira ndi kuwadula bwino mziduswa zing’onozing’ono
- Kapangidwe kake ndi chimodzi-modzi ndi wa pa dzenje. Onani zithunzi.
7
- Mulu utalike 1.0–1.5m, pansi tilembelele 1.5-2.0m ndipo mulitali mutengere kukula kwa
malo opangira manyowa.
1.5 - 2.0 m
3.0 m or more
1.0 - 1.5 m
8
- Tembenuzani mulu wanu pakatha masabata 2-3
- Onani ngati kompositi wanu akutentha
Kasungidwe ka kompositi
Kompositi amakhala atapsya pakatha masabata anai.Sungani kompositi wanu potsatira njira
izi:
� Onetsetsani kuti manyowa ali ndi chinyezi chokwana 35% mpaka nthawi yomwe
mukufuna kugwiritsa ntchito.
� Sungani manyowa pa mthunzi.
� Mukhoza kusunganso kompositi m’matumba.
Mmene mungagwiritsire ntchito manyowa
Manyowa mukhonza kugwiritsa ntchito ku mbeu zambiri
� Mukhonza kuthira ku mbeu zakumunda monga chimanga kapena za masamba
podzadza manja awiri pa dzenje lili lonse
� Mukhonza kudzadza manja ndi kuthira pa mulingo osapitilira 10cm
� Mukhonzanso kuthira mbali mwa mbeu zanu pansi penipeni
Manyowa omwe sanapsye kwenikweni mukhonza kuyala pansi pa mbeu zanu kapena pansi pa
mbeu za mitengo. Ndikoyenera kuvindikira manyowa oterewa ndi dzinthu zolimbirapo
kuwopesa kuti angauluke ndi mphepo.
� Manyowa mukhonza kuthira ku mbande zamitengo
� Mukhonzanso kuthira mmayiwe ansomba ngati zakudya za nsomba
Manyowa obiiriwira
Pa malimidwe, manyowa obiliwira ndi mbeu yomwe imadzalidwa mwadaladala kuti iphimbe
nthaka ndikudzakwiriridwa munthaka isanafike nthawi yoti ibeleke. Mbeuyi imawonjezera
mchere mu nthaka kudzera ku mizu ndi masamba ake amene amakwirilidwa. Mwachidule
ntchito zake ndi kubwezeretsa chonde munthaka komanso kuteteza nthaka. Ubwino wina wa
manyowa wobiliwila ndi uwu:
• Tizilombo tomwe timapezeka mu tizotupa/mandolo ta m’mizu ya mbeyu zomwe
zimadzalidwira ntchitoyi timapanga nitrogeni yemwe mbeu zina zimagwiritsa ntchito
pompo-pompo.
• Kupezeka kwa mpwyeya, madzi ndi zina munthaka kumakhala kwabwino chifukwa cha
masamba omwe amaolelana.
• Mbeu zimakoka zakudya za mbeu zomwe zili pansi pogwiritsa ntchito muzu wawo wozama.
• Mbeu yodzalidwa imachepetsa kameledwe ka udzu m’munda.
• Mbeu ngati yasiyidwa kuti ipange maluwa imakopa tizilombo tomwe timathandiza
kukhwimitsa mbeu.
9
Monga liulo likumvekera manyowawa amapangidwa kuchokera ku zomera zimene tsidzinaume
monga udzu, mbeu zina monga chimanga kapena mbeu za mtundu wa nyemba zomwe zidakali
zaziwitsi. Izi zimaphatikidzidwa kunthaka zisanayambe maluwa. Pakutha pa mwezi umodzi
kapena iwiri zimawola ndi kusanduka dothi mothandizidwa ndi tizirombo tingo’no-tingo’no
tosawoneka ndi maso athu. Manyowawa amathandiza kuteteza nthaka yathu kuti isakokoloke
ndi madzi. Komabe manyowawa amathanso kufalitsa matenda ku mbeu ngati zomwe
zapangidwira zili ndi matenda.
Chifukwa chiyani tiyenera kuthira manyowa?
Pambali popereka chonde ku nthaka yathu,manyowa amathandiza kubwezera nthaka ku
chilengedwe chake.Potero mpweya ndi madzi zimasungika bwino mu nthaka yanu,
powonjezera apo zakudya za mbeu zimasungika ndi kumadyetsera mbeu pango’no-pang’ono.
Manyowa amathandizanso nthaka yathu kuti ikhale yopanda nchere wambiri.
Table 4. Ubwino ndi kuipa kwa manyowa
Ubwino wa Manyowa Kuipa kwa Manyowa
� Manyowa ndi osavuta kupanga
komanso osakwera mtengo
� Amabwezeretsa chonde monga
mmene nthaka inapangidwira
� Amasunga madzi ngati siponje
� Amasunga tizirombo tina tamunthaka
� Manyowa amawonjezera ntchito zina
za tizirombo tamunthaka
� Alibe zakudya za mbeu zokwanira
� Amafunika kuthira ochuluka pa malo
ochepa
� Amafunika khama kuti atheke ndi
kuthira
� Amafunikira nthawi yabwino kuti
apangidwe
� Amapereka zakudya za munthaka
pango’no-pang’ono
10
INTRODUCTION
Soil depletion occurs when the components which contribute to fertility are removed and not
replaced and the conditions which support soil fertility are not maintained. This leads to poor
crop yields. In agriculture, depletion can be due to excessively intense cultivation and inadequate soil management.
In some places, soils have been depleted through rapid and almost total nutrient removal
because of the combined effects of growing population densities, of continuous cropping of
farmlands without proper soil conservation measures, of overtillage which damages soil
structure and of overuse of synthetic fertilizers and herbicides, which leave residues and buildups that inhibit microorganisms and salinization of soil.
Other means of soil rejuvenation, such as manure use must, therefore, be explored and
encouraged. The purpose of this training manual for soil conservation is to introduce
composting and other soil conservation practices to farmers in our villages.
Farmyard manure is the most commonly used organic fertiliser world wide. It demands
farming systems which permit effective collection of animal dropping. This can not be managed
with free roaming livestock. Only a proper and an integrated farm management with
appropriate animal housing facilities and manure collection, permits to make best use of these
valuable sources for the sake of improving soil fertility from farm own resources at low
external cost.
Soil fertility is maintained by putting back into soil the nutrients removed by crops or lost
through leaching and soil erosion. Once soil fertility is maintained for high crop yields, good
farming practices help to prevent loss of soil fertility and replace the nutrients that have been
lost.
11
CLASSIFICATION OF FERTILISERS
Fertilisers are substances which, when added to the soil, supply plant nutrients. Fertilisers can
be classified into two groups, namely inorganic or chemical fertilisers and organic fertilisers or
manure.
Inorganic or chemical fetilisers
Inorganic fertilizer is classified into straight fertilizer and mixed fertilizer.
Straight (or single) fertilisers:
Fertiliser containing single nutrient of nitrogen, phosphate or potassium (Urea,
Superphosphato, Potassiu Chloride)
Compound (or mixed) fertilisers:
Fertiliser containing more than double nutrients of nitrogen, phosphate or potassium.
Compound fertiliser is a form of mixed fertiliser, which contains all elements in one granule
(designated blended fertilisers, paste fertiliser, liquid fertiliser)
Meaning of numbers written on a bag of fertilizer
Each number shows the content ratio of nitrogen, phosphate and
potassium from left to right. This example shows that this pack of
fertiliser contains nitrogen, phosphate and potassium 14% each.
14-14-14 means that there is 42g of fertilizer elements in 100g content.
Advantages and disadvantages of inorganic fertilisers:
Advantages
- They contain a lot of nutrients
- They do not require a lot of
labour during application
- The supply of nutrients
iimmediate
- Nutrients are easily soluble
in the soil
Disadvantages
- They are dangerous for human
health
- They are expensive
- They may cause soil and water
pollution
- The soil may become acidic with
continued use
- Some of the nutrients may leach
- Some of the nutrients may become
fixed, e.g. phosphorus
- They do not improve soil structure
- Crops may be damaged if they are
not properly applied
12
Table 1. Some characteristics of straight fertilisers
Fertiliser Characteristics
Sulphate of Ammonia
21% N
- Soluble in water
- Makes soil acidic
- Does not leach easily
- Does not absorb moisture from the air
- Crystals are white and very fine, like sugar
Urea
46% N
- Readily dissolves in water
- Has no acid effect on the soil
- Acts quickly
- Absorb moisture from the air
- Granules are white
CAN
26-28% N + Calcium
- Soluble in water
- Helps to neutralise soil acidity
- Improves soil structure
- Absorbs moisture from the air
- Colour varies from yellow to brown
Single Super Phosphate
8.5% P2O5
- Soluble in water
- Insoluble in acidic soil
- Supplies sulphur
- Granules are creamy-white
Double Super Phosphate
45% P2O5
- Soluble in water
- Insoluble in acid soil
- Has no acid effect on the soil
- Granules are grey
Sulphate of Potash
40% K2O
- Very soluble in water
- Does not leach
- Granules are fine like salt and yellowish
Muriate of Potash
60% Potash K2O
- Very soluble in water
- Does not leach
13
ORGANIC FERTILISERS
Farm Yard Manure (FYM)
It is sometimes called kraal or khola manure.
This is the traditional manure and is mostly readily available to the farmers. Farm yard manure
is a decomposed mixture of Cattle dung and urine with straw and litter used as bedding
material and residues from the fodder fed to the cattle.
The sources of farmyard manure include sheep, cattle, goats, pigs, and poultry. The manure is
rich in nitrogen (N) and potassium (K) but has very little phosphorus (P). The quality of
farmyard manure depends on the type of animal, the age of the animal, the kind of feed given
to the animals, the kind of litter used, the age of the manure and method of storage.
Table 2. Factors that affect the quality of farmyard manure (FYM)
Factor Effect
Type of animal Animals fed on concentrates such as
fattening animals produce rich manure
Age of the animal
Young animals use up most of the nutrients
in the feed. Old animals, therefore, produce
better manure.
Type of feed given to animals
The richer the feed in terms of
carbohydrates, proteins and other
minerals, the richer the manure will be
Type bedding material used
• Litter which is able to absorb a lot of
urine and can easily decompose
produces good quality manure
• Some litter may be poor in itself,
eg. Saw dust, maize stover, etc
• Stalks and wood shavings do not
decompose easily to produce good
manure
• Othe materials that are rich in
nutrients such as elephant grass,
produce good quality manure.
Elephant grass is rich in nitrogen
and phosphorous. However, it does
not absorb a lot of urine
Age of farmyard manure
• Old and well-rotted farm yard
manure is rich in nutrients
• Farmyard manure should be given
enough time to rot before it is used
Method of storage Farmyard manure should be stored under a
shed to prevent nutrients from leaching
Compost
Compost is simply decomposed organic material. The organic material can be plant material or
animal matter. While composting may seem mysterious or complicated, it’s really a very
simple and natural process that continuously occurs in nature, often without any assistance
from mankind.
Both living plants and annual plants that die at the end of the season are consumed by animals
of all sizes, from larger mammals, birds, and rodents to worms, insects, and microscopic
organisms. The result of this natural cycle is compost, a combination of digested and
undigested food that is left on the forest floor to create rich, usually soft, sweet-smelling soil.
Compost is good for two very compelling reasons. It’s great for the garden/field, and it’s
environmentally responsible.
14
Garden benefits
Compost is great for the garden because it improves the soil, which in turn supports healthier
and more productive plants. Compost provides virtually all of the essential nutrients for
healthy plant growth and it almost always releases those nutrients over time to give plants a
slow, steady, consistent intake of the elements essential for growth. Compost also improves
the soil’s structure, making it easier for soil to hold and use the right amount of moisture and
air. Compost will improve the texture of both clay and sandy soil; indeed, compost is the best
additive to make either clay or sandy soil into rich, moisture holding, loamy soil. And, as an
added benefit, compost improves plant vigor and provides for improved immunology from
diseases.
Environmental benefits
The most obvious environmental benefit is that composting can significantly reduce the
amount of solid waste. Clearly, the more we compost, the less we contribute to the cost of
trash removal and the volume of solid materials in landfills.
Using compost to feed your field and garden will also reduce your dependency on
chemical fertilisers. So, you’ll save money and reduce – if not eliminate - the
potential of chemical pollution to your little piece of the environment.
Using compost instead of chemical fertilisers will ensure that your field and garden thrive in
soil that is alive and healthy.
The best compost can be made if the following factors are combined well: type of material, air,
moisture, temperature, soil acidity (pH).
Ingredients in compost
To prepare the compost, two classes of materials are needed, simply referred to as “Greens” or
fresh and “Browns” or dry. Green materials are high in nitrogen, while brown materials are
high in carbon. The green materials provide protein for the microbes while the brown materials
provide energy.
Typical green materials are:
• Fresh (green) Grass clippings
• Fresh manure (horse, chicken, rabbit, cow)
• Kitchen scraps (fruit, vegetables, coffee grounds, tea bags)
• Weeds
• Green leaves
• Leftover fruits from the garden
Typical brown materials include:
• Brown, dry leaves
• Dried grass
• Cornstalks (shredded)
• Straw
• Sawdust (in moderation)
Some materials are NOT REQUIRED. See the table below:
15
Table 3. Materias that can and cannot be added to a compost pile
Yes No
High Nitrogen Plant sprayed with chemicals
Animal manure Diseased plant material
Aquitic weeds i Metal pieces
Bread Plastic material
Egg shells Fatty food wastes
Fruit peels and rinds Dog or cat manure
Legume leavesi
Leguminous leaves
Grass clippings
High Carbon
Dry weeds
Paper
Saw dust
Wood ash
Straw
Wood chips
Compost preparation
There are two methods of compost preparation. These are:
� Deep Bed Method
� The Open Heap Method
Deep Bed Method is recommended for dry regions or for dry seasons.
The draft below illustrates the process:
Pit dimensions - 2-2.5 m long, 1.2-2 m wide and dig 60 cm deep.
Place chopped dry materials that are difficult to rot at the base of one pit. The level should be
10 cm thick.
16
Then sprinkle water on it.
- Add 10cm thick layer of fresh materials such as
vegetable waste or fresh weed;
- Sprinkle about 10 handfuls of wood ash;
- Spread 2cm thick of animal manure or old compost on
it;
- Spread 1cm thick topsoil;
- Water the pile well.
- Repeat all the layers except the first layer of coarse
materials until the heap is full to about 20-30cm above
ground level;
- Water the whole heap well;
- Cover the heap with grass, banana or plantain leaves;
- Push a long stick diagonally into the compost heap to help
check temperature;
- Remouve the long stick to verify the temperature.
- If the stick is cold (after 2-3 weeks), turn the layers
upside down in the second area;
- Start to feel again the first area following the same
rules, while the second one is breaking down.
After 4 weeks the compost is ready, when the stick is cold again.
Open Heap Method is the
same except that a pit is not
dug and these following rules
must be respected:
17
- First a good quantity of stems (millet or corn) has tobe collected and cut into small pieces;
- All materials must be well mixed and sprinkled before the heap preparation, as shown in the
following drawings:
- First collect stems (millet or corn) and cut them into small pie
c
- The height of the heap should be 1.0–1.5m, the base at least 1.5-2.0m and the length
according to the available space. It is recommended to use a fork making and turning the
heap.
18
- The temperature must be kept under control with a long stick as in the Deep bed method
waiting for the heap turning (after 2-3 week);
- It is recommended to test the heap each week to make sure that it is neither too dry nor too
wet;
- After 2-3 weeks, if the stick is cold, the heap should be
turned upside down removing it from one side to the
other;
- A second heap can be done while the second one is
breaking down;
- After 4 weeks the first heap is ready to be stored or to
collect for fields crops;
- All residual fluids can be used as liquid fertiliser.
STORAGE COMPOST
The compost is ready after 2-3 months from the day it was started.
The storage process is described below:
Maintain the compost wet at approximately 35% until required
Store compost in a shady place until required
Compost can also be put in sacks and stored under shade till it is needed for use
How to use compost
Compost can be used for many crops:
� You can put a handful of compost into planting holes for fields’ crops like corn or
vegetables.
� You can mix it into the top 10cm of your soil.
� You can also put it at the base of your plants.
Semi decomposed compost can be used as mulch between crops or around trees. It is
advisable to cover such mulch with straw to avoid loss of nutrient.
1.5 - 2.0 m
3.0 m or more
1.0 - 1.5 m
19
� Compost can be mixed with soil for raising tree seedlings
� It can be used as fish feed.
Green manure
In agriculture, a green manure is a type of cover crop grown primarily to add nutrients and
organic matter to the soil. Typically, a green manure crop is grown for a specific period and
then plowed under and incorporated into the soil. Green manures usually perform multiple
functions that include soil improvement and soil protection:
• Leguminous green manures contain nitrogen-fixing symbiotic bacteria in root nodules
that fix atmospheric nitrogen in a form that plants can use;
• Green manures increase the percentage of organic matter (biomass) in the soil, thereby
improving water retention, aeration, and other soil characteristics;
• The root systems of some varieties of green manure grow deep in the soil and bring up
nutrient resources unavailable to shallower-rooted crops;
• Common cover crop functions of weed suppression and prevention of soil erosion and
compaction are often also taken into account when selecting and using green manures;
• Some green manure crops, when allowed to flower, provide forage for pollinating
insects.
As the term suggests, green manure is a type of manure made from plants, such as weeds,
grasses, maize and other leguminous plants which are still green. The plants are incorporated
into the soil at flowering stage. They, then, after 1 or 2 months, decompose through the action
of bacteria and other organisms, and turn into humus. Humus improves the structure of the
soil and provides it with nutrients.
Why organic fertilizers
Apart from supplying nutrients to the soil, organic fertilisers improve soil structure. In this
way, drainage, aeration and water holding capacity are improved. In addition, the nutrients
are released at a steady rate. Organic fertilisers will also modify the soil temperature and its
acidity.
Table 4. Advantages and disadvantages of manure
Advantages of manure Disadvantages of manure
� Organic fertilisers are cheap and easy
to make
� They improve soil structure by
supplying humus to the soil
� They improve soil drainage and
aeration
� They are good source of micro-
nutrients
� They improve the activity of microbes
in the soil
� They are low in nutrients. For example,
Farm Yard Manure (FYM) is low in
Phosphorus
� A lot of manure is required per unit
area
� A lot of labour is required during
application
� It demands a lot of time and
commitment to make
� They release nutrients slowly