36
Kubala Zipatso mu Uthenga Wabwino Maphunziro asanu ndi awiri amu buku la Akolose

Colossians bible studies chichewa

Embed Size (px)

DESCRIPTION

Seven Bible Studies in Chichewa on the book of Colossians

Citation preview

Page 1: Colossians bible studies chichewa

Kubala Zipatso mu Uthenga Wabwino

Maphunziro asanu ndi awiri amu buku la Akolose

Page 2: Colossians bible studies chichewa

2

Front Cover Photo: Zombwe, Northern Region of Malawi

Page 3: Colossians bible studies chichewa

3

Kubala Zipatso mu Uthenga Wabwino

Maphunziro asanu ndi awiri amu buku la Akolose

Page 4: Colossians bible studies chichewa

4

Bearing Fruit in the Gospel Seven Bible Studies through Colossians

(Chichewa Edition, 2014)

Written by: Peter Ong

Translated by: Mrs Fanny Kapakasa

Reviewed by:

Rev. Chisoni Bridge

Rev. Wabwinondani Chamambala

Mrs Jacky Hammond

Rev. Action Majawa

Rev. Louis Ndekha

Mr Luke Voight

Mr Steven Wheatley

Published by:

The Africa Evangelical Church

PO Box 2390, Blantyre, MALAWI

Printed by:

Assemblies of God Press

PO Box 5749, Limbe, MALAWI

Unless otherwise stated all Scripture text is taken from:

Buku Loyera, copyright 1998 by the Bible Society of Malawi. Used by permission.

All rights reserved. Except as may be permitted by the Copyright Act, no part of this publica-

tion may be reproduced in any form or by any means without prior permission from the pub-

lisher.

Front and Back Cover Design by: Peter Ong and John Kwok

A Publication of:

Page 5: Colossians bible studies chichewa

5

Poyamba

Cholinga cha maphunziro awa ochokera mu buku la Akolose ndi kulimbikitsa kukula mu uzi-

mu pakati pa achinyamata mu mpingo wa Africa Evangelical (AEC) ndiponso kunja kwa

mpingowu pamene aphunzira ndi kumvetsetsa mau a Mulungu pa iwo wokha.

Ku Malawi lero, kuli zolankhula zambiri zopikisana zimene zimafotokozera achinyamata za

zinthu zofunikira pa moyo, ndipo ambiri amatengeka kutsatira njira ya ku chiwonongeko

chifukwa anamizidwa. M’malo motengeka ndi maganizo osathandiza a anthu kapena a dziko

lapansi (Akolose 2: 8), achinyamata ayenera kudziwa ndi kukula mu Uthenga Wabwino -

Uthenga Wabwino wakuti Yesu akuwapatsa mwayi wa chikhululukiro, ubale ndi Mulungu,

moyo watsopano ndiponso cholinga chake kudzera mu imfa ndi kuuka kwake.

Kalata ya Paulo kwa Akolose ili ngati uthenga wa nthawi zonse kwa achinyamata a lero kuti

Yesu ndi munthu wofunikira kwambiri choncho iwo ayenera kumudziwa komanso ku-

mumvera. Chifukwa chiyani? Paulo akunena mu Akolose 1: 15-16:

Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye Mwana wake

woyamba, wolamulira zolengedwa zonse. Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse

zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu,

aulamuliro ndi amphamvu ena onse.

Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo.

Yesu ndi wofunikira kwambiri padziko lonse lapansi. Achinyamata analengedwera iye. Chon-

cho cholinga cha moyo wawo chimapezeka ndi kukhazikika mwa IYE! Iye ndiye mau ofunikira

amene ayenera kuwamvera m’malo mwa mau ambiri opanda phindu a m’dziko lapansi ame-

ne amapikisana naye pa chikoka chawo.

Ndi chikhumbokhumbo cha AEC ndi SIM kuona kuti uthenga wa Mulungu ukubala chipatso

ndipo ukukula pakati pa achinyamata a ku Malawi (Akolose 1:6) kuti iwo akayende mu njira

yoyenera ya Yesu, kubereka chipatso mu ntchito ili yonse yabwino ndi kukula muchidziwitso

cha Mulungu (Akolose 1:10). Choncho maphunziro a Baibulowa, akhazikika pa mutu wa

“kubala chipatso mu Uthenga Wabwino”.

Maphunziro asanu ndi awiri (7) mu kabuku aka ndi awa:

1:1-14 Uthenga Wabwino ndi chiyani?

1:15-23 Kodi Yesu ndi wofunikira chifukwa chiyani?

1:24-2:5 Kodi timakula bwanji mu moyo wathu wa uzimu?

2:6-23 Osanamizidwa ndi m’mene dziko lapansi limaganizira!

3:1-17 Moyo wosinthika

3:18-4:1 Ubale wosinthika

4:2-18 Cholinga chatsopano

Page 6: Colossians bible studies chichewa

6

Phunziro lililonse lili ndi ndime ya mu Baibulo pa Akolose ndipo phunziro lililonse lagawidwa

mundondomeko zothandiza achinyamata kutulukira pa okha mau a Mulungu pamene afufuza

za ndimezi ndi kumvetsa tanthauzo lake lenileni ndi m’mene angaligwiritsire ntchito kwa iwo

eni m’moyo wa lero.

Mau oyamba a phunziro: Afotokozera mwachidule za ndime ya mu

Baibulo ndi mutu wa phunziro.

Tiyeni ticheze: Funso loyambira lolimbikitsa achinyamata

kulankhula.

Tiyeni tiwone zimene ndime ikunena: Mafunso okonzedwa kulimbikitsa achinya-

mata kudziwa bwino ndime.

Tiyeni timvetse zimene ndime ikutanthauza: Mafunso okonzedwa kumasulira ndime.

Tiyeni tigwiritse ntchito ndime: Mafunso okonzedwa kuthandiza achinya-

mata kudziwa m’mene angagwiritsire ntchi-

to zimene aphunzirazo mu miyoyo yawo

Phunziro mu nkhani yochitika: Nkhani yochitika imaperekedwa kwa

achinyamata kuti akambirane m’mene iwo

angathandizire. Ndiyokonzedwa molingana

ndi zonse zimene aphunzira.

Mfundo yaikulu mu phunziro: Ifotokozera mfundo yaikulu mu phunziro

kuti achinyamata adzatengere kwao

m’maganizo awo.

Tiyeni tipemphere: Chikumbutso kwa achinyamata

kupempherera zimene aphunzira, ku-

mupempha Mulungu kuti abweretse kusin-

tha, kukula ndiponso chipatso mu gawo ili la

phunziro.

Page 7: Colossians bible studies chichewa

7

KALATA YA PAULO YOLEMBERA

AKOLOSE

Mau Oyambirira

Kolose unali mzinda wina wa ku Asiya, kuvuma kwa Efeso. Si ndiye Paulo adayambitsa mpingo kumeneko, komabe amausamala, poti adatuma anthu ake ku Koloseko kuchokera ku Efeso. Paulo adaamva kuti aphunzitsi ena onyenga aku-sokoneza mpingo umenewo; iwo akuti ofuna kumdziŵa Mulungu ndi kupulumuka ayenera kupembedza mafumu ndi akuluakulu akumwamba, ayeneranso kuumbalid-wa ndi kutsata miyambo ndi malamulo ena okhudza zakudya ndi zina zotere. Tsono Paulo aŵalembera kalatayi kuti atsutse zabodzazi pofotokoza uthenga weniweni Wachikhristu, makamaka zakuti Yesu Khristu yekha ali ndi mphamvu zopulumutsa anthu, koma zimene amalalika aphunzitsi aja zimangosokoneza anthundi kuŵalekanitsa ndi Khristu. Mulungutu adalenga zinthu zonse kudzera mwa Khristu ndipo amabwezera zonsezo kwa Iye mwini wake kudzera mwa Khristu yemweyo. Anthu a pa dziko lonse lapansi angayembekeze kupulumuka pokhapo atakhala mwa Khristu ndi kuphatikana naye. Zotsatira zake nzakuti iwowo aongolere moyo wao potsata zomwe iye Paulo akuŵaphunzitsazi. Potuma Titiko ku Filipi kuti akapereke kalatayi, Paulo anatumanso mnyamata wina womperekeza, dzina lake Onesimo; ameneyu ndiye kapolo uja amene nkhani yake imapezeka m'kalata yomwe Paulo adalembera Filemoni.

1. Mau oyamba (1.1-8) 2. Za makhalidwe ndi ntchito za Khristu (1.9--2.19) 3. Za moyo watsopano wokhala mwa Khristu (2.20--4.6) 4. Mau otsiriza (4.7-18)

1 Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndili limodzi ndi Timoteo, mbale wathu.

2 Tikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu okhala ku Kolose, abale athu okhulupirika mwa Khristu.

Mulungu Atate athu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.

Paulo ayamika Mulungu chifukwa cha akhristu a ku Kolose 3 Tikamakupemphererani, nthaŵi zonse timathokoza Mulungu, Atate a Ambuye athu

Yesu Khristu. 4 Timathokoza chifukwa tamva kuti mumakhulupirira Khristu Yesu, ndiponso kuti mumakonda anthu onse a Mulungu. 5 Gwero la zonsezi ndi chiyembekezo chimene muli nacho chodzalandira zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Mudamva za zime-nezi pamene mau oona, adakufikani poyamba paja. Mau oonawo ndi Uthenga Wabwino. 6 Uthenga Wabwinowu ukubala zipatso ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi, monga mom-we wachitiranso pakati panu, kuyambira tsiku limene mudamva ndi kumvetsa za kukoma mtima kwa Mulungu. 7 Mudaphunzira zimenezi kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokonded-wa. Iye uja akugwirira ntchito Khristu mokhulupirika m'malo mwathu. 8 Ndiye amene adati-dziŵitsa za chikondi chomwe Mzimu Woyera adaika mwa inu.

1

Page 8: Colossians bible studies chichewa

8

Paulo apempherera akhristu a ku Kolose 9 Nchifukwa chake, kuyambira tsiku limene tidamva zimenezi, sitileka kukupempherera-

ni. Timapempha Mulungu kuti akudzazeni ndi nzeru ndi luntha, zimene Mzimu Woyera amapatsa, kuti mumvetse zonse zimene Iye afuna. 10 Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjeze-rawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.

11 Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yaulemerero, kuti muzipirira zonse ndi mitima yoleza ndi yosangalala. 12 Ndipo timapemphera kuti muziyami-ka Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungi-ra anthu ao mu ufumu wa kuŵala. 13 Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkuti-loŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. 14 Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.

Za makhalidwe ndi ntchito za Khristu 15 Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye Mwana wake woyamba, wolamulira zolengedwa zonse. 16 Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo. 17 Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi. 18 Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, Woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu. 19 Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo. 20 Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.

Page 9: Colossians bible studies chichewa

9

21 Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'nt-

chito zanu zoipa. 22 Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulun-gu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwon-eka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse. 23 Koma tsono muzikha-la okhazikika kolimba pa maziko a chikhulupiriro chanu, osasunthika pa chiyembekezo chofumira ku Uthenga Wabwino umene mudamva. Uthenga Wabwinowu walalikidwa kwa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo Mulungu ndiye adandipatsa ine, Paulo, ntchito yoti ndiwulalike.

Za m'mene Paulo akutumikira mpingo 24 Tsopano ndakondwa kuti ndikukuvutikirani. Pakuti pakumva zoŵaŵazo, ndikutsiriza

m'thupi mwanga zotsala za masautso a Khristu kuthandiza thupi lake, ndiye kuti Mpingo. 25 Ndipo ine ndine mtumiki wa Mpingowu, pakuti Mulungu ndiye adandipatsa ntchitoyi yoti ndikulalikireni kwathunthu mau ake. 26 Mauwo ndi chinsinsi chozama chimene chinali cho-bisika chikhalire kwa mibadwo yonse, koma tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake. 27 Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziŵitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero. 28 Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu. 29 Ndi cholinga chimenechi ndikugwiradi ntchito kwambiri ndi mphamvu ya Khristu imene ikugwira ntchito kolimba mwa ine.

1 Ndikufuna kuti mudziŵe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo ndi anzanu a ku Laodikea, ndi ena onse amene sitidaonane nawo maso ndi maso chikhalire. 2 Ndikufuna kuti zimenezi ziŵalimbitse mtima, ndipo azilunzana pamodzi m'chikondi, azikhala odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu. Motero adzatha kudziŵa mozama chinsinsi cha Mulungu chonena za Khristu. 3 Mwa Iyeyu mudzapeza chuma chonse chobisika, ndiye kuti nzeru ndi luntha.

4 Ndikunenatu zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense angakukopeni ndi mau onyenga. 5 Pakuti ngakhale sindili nanu m'thupi, komabe mumtimamu ndili nanu pamodzi. Ndipo ndakondwa kuwona kuti mukulongosola bwino zonse, ndi kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu nchosagwedezeka konse.

Za moyo weniweni pakukhala mwa Khristu 6 Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu

wonse ukhale wolunzana naye. 7 Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.

8 Chenjerani kuti wina aliyense angakusokonezeni ndi mau olongosola nzeru zapatali. Ameneŵa ndi mau onyenga chabe. Paja nzeru zimenezi zimangochokera ku miyambo ya anthu, ndi ku maganizo ao okhudza zapansipano, osati kwa Khristu ai. 9 Pakuti m'thupi la Khristu umulungu wonse umakhalamo wathunthu. 10 Ndipo mwa Iye inu mudapatsidwa moyo wonse wathunthu. Iye ndiye mutu wolamulira maulamuliro onse ndi mphamvu zonse zosaoneka.

2

Page 10: Colossians bible studies chichewa

10

3

11 Mwa Iye mudachita ngati kuumbalidwa, osatitu kuumbala kwa anthuku ai, koma kuvu-la khalidwe lanu lokonda zoipa; kuumbala kumene amachita Khristu nkumeneku. 12 Pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m'manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa. 13 Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu zonse. 14 Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda. 15 Motero mwa Khristu Mulungu adaŵalanda zida maufumu ndi maulamuliro onse, ndipo pamaso pa onse, adaŵayendetsa ngati akaidi pa mdipiti wokondwerera kupambana kwake.

16 Wina aliyense asakuzengeni mlandu pa nkhani yokhudza zakudya kapena zakumwa, kapena pa zokhudza masiku a chikondwerero, kapena a mwezi wokhala chatsopano, kapena pa zokhudza tsiku la Sabata. 17 Zonsezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zen-izeni zimene zilikudza, koma zenizenizo ndi Khristu amene. 18 Wina aliyense asakuletseni kupata mphothoyo. Iwo aja amakonda kudziwonetsa ngati odzichepetsa, popembedza amatamanda angelo. Amaika mtima pa zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amadzitukumula popanda chifukwa, popeza kuti amangotsata nzeru za anthu, 19 osakangamira Khristu amene ali mutu wa Mpingo. Komatu mwa Khristu thupi lonse lima-landira mphamvu, ndi kulumikizika pamodzi mwa mfundo zake ndi mitsempha yake. Mot-ero thupi limakula monga momwe Mulungu afuna kuti likulire.

Za kufa ndi kuuka pamodzi ndi Khristu 20 Mudafa pamodzi ndi Khristu, ndiye kuti simulamulidwanso ndi miyambo ya dziko

lapansi. Tsono bwanji mukuchita ngati kuti moyo wanu ukudalirabe zapansipano? Bwanji mukuŵamvera malamulo onga aŵa akuti, 21 “Usagwire chakuti”, “Usakhudze chakuti”? 22 Malamulo ameneŵa ndi zophunzitsa zimenezi ndi za anthu chabe, ndipo zimangokhudza zinthu zimene zimatha, anthu akamazigwiritsa ntchito. 23 Kwinaku mauwo amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamula anthu zambiri pa za kupembedza, za kudzichepetsa ndi za kuzun-za thupi lao. Komabe malamulowo alibe phindu, ndipo sathandiza konse kugonjetsa khalid-we longosangalatsa thupi.

1 Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kum-

wamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. 2 Muzifunafuna za Kum-wamba, osati zapansipano. 3 Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. 4 Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ule-merero pamodzi naye.

Page 11: Colossians bible studies chichewa

11

Za moyo wakale ndi watsopano 5 Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama,

zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbom-bo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano. 6 Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amaŵakwiyira anthu osamumvera. 7 Inunso kale makhalidwe anu anali omwewo, munkachita zomwezo.

8 Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mi-jedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa. 9 Musamauzana mabodza, pakuti mwachita ngati mwavula moyo wanu wakale, pamodzi ndi zochitachita zake zoipa, 10 ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. 11 M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. 12 Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani,

muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. 13 Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga

Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. 14 Kuwonjezera pa zonsezi

muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. 15 Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti

mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala

oyamika. 16 Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi

kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pame-

ne mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. 17 Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite

m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

Za moyo watsopano m'banja 18 Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. 19 Inu

amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. 20 Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye.

21 Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, kuti angataye mtima. 22 Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu

zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye. 23 Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mti-ma wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. 24 Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu. 25 Koma munthu amene amachita zosalungama, zidzamubwerera, chifukwa Mulungu amaweruza mosakondera.

_____________ 3.10: Gen. 1:26,27

Page 12: Colossians bible studies chichewa

12

4

1 Inu ambuye, antchito anu muzikhalitsana nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziŵa kuti inunso muli ndi Mbuye wanu Kumwamba.

Malangizo ena 2 Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndipon-

so oyamika Mulungu. 3 Ifeyonso muzitipempherera kuti Mulungu atipatse mwai woti tilalike mau ake, makamaka kuti tilengeze chinsinsi chozama chokhudza Khristu. Chifukwa cha kulalika chinsinsichi ndine womangidwa m'ndende muno. 4 Mundipempherere tsono kuti ndichifotokoze bwino monga ndiyenera.

5 Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe. 6 Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti po-tero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.

Mau otsiriza 7 Tikiko, mbale wathu wokondedwa, adzakudziŵitsani zonse za ine. Iyeyo ndi mtumiki

wokhulupirika, wantchito mnzathu pa ntchito ya Ambuye. 8 Nchifukwa chake ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti adzakulimbitseni mtima. 9 Ndikumtuma pamodzi ndi Onesimo, mbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali mmodzi mwa inu. Iwo adzakudziŵitsani zonse zakuno. 10 Aristariko, mkaidi mnzanga, akukupatsani moni. Akuteronso Marko, msuweni wa Bar-

nabasi. Za Markoyo mudalandira kale mau akuti akafika kwanuko, mumlandire bwino. 11 Akutinso moni Yesu, wotchedwa Yusto. Mwa ochokera ku Chiyuda ndi atatu okhaŵa

amene akundithandiza pa ntchito ya Ufumu wa Mulungu, ndipo andilimbikitsa kwambiri.

12 Akukupatsani moni Epafra, amene ali mmodzi mwa inu, ndiponso mtumiki wa Khristu

Yesu. Nthaŵi zonse iyeyo amalimbikira kukukumbukirani m'mapemphero ake. Amatero

pofuna kuti inuyo mukhale okhazikika, angwiro, ndipo kuti muzichilimikira kuchita zonse

zimene Mulungu afuna. 13 Ndingathe kumchitira umboni kuti amagwira ntchito kwambiri

chifukwa cha inu, ndiponso chifukwa cha anthu okhala ku Laodikea ndi ku Hierapoli. 14 Luka, sing'anga wathu wokondedwa, ndiponso Dema, onsewo akuti moni.

15 Mutiperekereko moni kwa abale athu okhala ku Laodikea, ndiponso kwa Nimfa ndi kwa ampingo amene amasonkhana kunyumba kwake. 16 Kalatayi itaŵerengedwa pakati panu, ikaŵerengedwenso mu mpingo wa ku Laodikea. Ndipo inunso muŵerengeko kalata imene a ku Laodikea adzakutumizirani. 17 Uzani Arkipo kuti, “Samala bwino kuti ntchito imene Ambuye adakupatsa uziigwira moikapo mtima.”

18 Ndi dzanja langalanga ndikulemba mau aŵa: “Moni. Ndine Paulo.” Kumbukirani kuti ndili m'maunyolo. Mulungu akukomereni mtima.

Page 13: Colossians bible studies chichewa

13

Phunziro 1 - Uthenga Wabwino ndi chiyani?

Ndime yophunzira ya m’Baibulo: Akolose 1:1-14

Mau oyamba a phunziro:

Kukolola chimanga chambiri chaka ndi chaka kumatengera kubzala mbeu yabwino mu ntha-

ka yabwino ndiponso madzi ambiri ndi dzuwa. Munjira yomweyo, Paulo mtumiki ndi mpingo

woyamba anabzala mbeu yabwino ya Uthenga Wabwino kulikonse kumene Mulungu anawa-

tuma. Pansi pa utsogoleri wa Mulungu, Uthenga Wabwino unayamba kukula ndi kubala

chipatso ku malo amenewa. Amodzi mwa malowa ndi ku Kolose.

Ndime yalero ndi yotsegulira kalata ya Paulo kwa Akolose m’mene muli malonje, pemphero

ndi kuthokoza kwa Mulungu chifukwa cha Akolose. Mukutsegulira uku, Paulo akuyamikira

Mulungu chifukwa cha kukula kwa Uthenga Wabwino kudziko komanso pakati pa Akolose.

Phunziro ili ndi la kumvetsa kuti Uthenga Wabwino ndi chiyani, ndiponso kusintha kumene

uthengawu umapanga m’miyoyo yathu.

Tiyeni ticheze:

Kodi mungadziwe bwanji kuti mtengo wa mango ukukula bwino kapena ayi?

Chimodzimodzi anthu amadziwa kuti ndife akhristu kapenanso kuti tikukula bwino ngati

Akhristu chifukwa cha chipatso chimene chimatuluka mu miyoyo yathu. Tiyeni tiwonetsetse

ndime ya lero ya mu Baibulo ndipo tione zimene tingaphunzire za kubala chipatso mu

Uthenga Wabwino mu miyoyo yathu.

Tiyeni tiwone zimene ndimeyi ikunena:

1) Kodi Paulo anayamba bwanji kalata yake kwa Akolose? (vv.1-3)

2) Kodi Paulo akuthokoza Mulungu pa chiyani chifukwa cha Akolose? (vv.3-5)

3) Kodi Uthenga Wabwino unabwera bwanji kwa Akolose; ndipo Paulo anamva bwanji

za kupita patsogolo mu chikhulupiriro ndi chikondi kwa Akolose? (vv. 5- 8)

4) Kodi Paulo akupempherera mosalekeza zinthu ziti zokhudza Akolose? (vv. 9 -14)

Page 14: Colossians bible studies chichewa

14

Tiyeni timvetse zimene ndimeyi ikutanthauza:

5) Kodi pali ubale wotani pakati pa chikhulupiriro cha Akolose mwa Yesu, chikondi

chawo kwa okhulupirira ndi chiyembekezo chawo kumwamba? (vv. 4-5) Kodi

chiyembekezo ichi chikuchokera kuti? (v.5)

6) Kodi mungadziwe bwanji kuti Akolose amvetsetsadi Uthenga Wabwino? (v.6) Kodi

ndi zipatso zotani zinaoneka m’miyoyo yawo? (Unikirani funso lapamwambapa)

7) Kodi ndi chifukwa chiyani Paulo akupemphera kuti Akolose adzadzadzidwe ndi

chidziwitso cha chifuniro cha Mulungu? (vv. 9-11)

Tiyeni tigwiritse ntchito ndimeyi:

8) Kodi munganene kuti Uthenga Wabwino ndi chiyani? Unikirani ma vesi awa 12-14.

9) Kodi achinyamata amene ali kunja kwa mpingo amaganiza chiyani za khalidwe ndi

kaganizidwe ka anthu mu tchalitchi? Kodi angaganize kuti khalidwe lawo ndi kaganiz-

idwe kawo kanasinthika ndi Uthenga Wabwino? Zili choncho kapena sizili choncho

chifukwa chiyani?

Page 15: Colossians bible studies chichewa

15

Phunziro mu nkhani yochitika:

Precious ndi m’modzi wa oyimba kwaya ya achinyamata ku tchalitchi. Iye wakhala akupita

kutchalitchi kwa nthawi yaitali koma sakudziwa bwino bwino kuti kukhala mkhristu ndi ku-

tani kupatula kuyimba mu kwaya. Samadziwa Kuti Uthenga Wabwino ndi chiyani kapena

kufunikira kwa Uthenga Wabwino ndi kotani pa moyo wake. Ngati Mnzake, inu mwakhala

mukuwerenga ndime iyi mu Akolose, kodi mungamuthandize bwanji?

Mfundo yaikulu mu phunziro:

Uthenga Wabwino ndi nkhani yabwino ya Mulungu imene anatipulumutsira ife ku moyo wa

ukapolo wa tchimo ndi kutibweretsa ife ku moyo wa mtendere mwa ubale ndi iye kudzera

mu imfa ya Yesu ndi kuuka kwake. Kwa iwo amene analapa ndipo anayika chikhulupiriro

chawo mwa Yesu, ndife mnzika zatsopano mu ufumu wa Mulungu, moyo watsopano ko-

manso chiyembekezo chatsopano. Choncho, kuganiza kwathu, malingaliro anthu, makhalid-

we athu ndipo maubale athu ayenera kuwonetsera ubale wathu watsopano ndi Mulungu.

Tiyeni tipemphere:

Thokozani chifukwa cha Uthenga Wabwino kuti Mulungu watiwombola ife ku imfa ndipo

watipatsa moyo watsopano. Thokozani kuti Uthenga Wabwinowu ukusintha miyoyo pa dziko

lapansi. Pempherani kuti Uthenga Wabwino udzasinthe miyoyo mu gulu lanu la achinyamata

ndiponso mu moyo wanu. Mupempheni Mulungu kuti akudzadzeni ndi chidziwitso cha

chifuniro chake kuti mungayende moyenera iye, kumusangalatsa iye, ndi kubala chipatso mu

ntchito ili yonse yabwino.

Page 16: Colossians bible studies chichewa

16

Phunziro 2 – Kodi Yesu ndi wofunikira chifukwa chiyani?

Ndime yophunzira ya m’Baibulo: Akolose 1:15-23

Mau oyamba a phunziro:

Paulo wasiya malonje ake kuthokoza ndi kupempherera Akolose ndipo wayamba kulemekeza

Yesu amene wawaombola ku mphamvu ya mdima ndi kuwapititsa ku dziko lowala komanso

kuwakhululukira machimo (1:13-14).

Ndime iyi ili ngati nyimbo yotamanda Yesu chifukwa cha mmene iye alili ndiponso chifukwa

cha zimene iye watichitira ife. Kutii tikule ndi kubala chipatso m’ moyo wathu wachikhristu,

tiyenera kukula pa kumvetsetsa kwathu kwa Uthenga Wabwino – ‘Nkhani Yabwino’ ya Yesu

ndi zomwe watichitira ife.

Yesu Khristu ndiye Uthenga Wabwino. Uthenga Wabwino umanena za Iye. Iye ndi wofunikira

kwambiri pa chikhulupiriro chathu.

Tiyeni ticheze:

Kodi ndi timu iti ya mpira wa miyendo kapena wa ntchemberembaye imene mu-

maikonda kapena woimba kaya ndi ndani amene mumamutsata? Chifukwa chiyani ?

Kodi mumadziwa zochuluka bwanji za timuyo kapena munthuyo?

Mu njira yomweyo timasangalarira timu ya pamtima pathu kapena munthu wa pamtima

pathu ndipo timafuna kuidziwa bwino kapena kumudziwa bwino, ngati akhristu, tiyenera

kutamanda Yesu ndi kufuna kumudziwa bwino. Choncho tiyeni tionetsetse ndime ya mu

Baibulo ya lero ndipo tiwone chimene tingaphunirepo cha Yesu.

Tiyeni tiwone zimene ndimeyi ikunena:

1) Pangani m’ndandanda wa zinthu zonse zimene Paulo anena za Yesu kuti ndi ndani

ndipo wapanga chiyani kwa Akolose? (vv. 15-23)

2) Kodi ubale wa Akolose ndi Mulungu unali wotani asanakhale Akhristu? (v.21)

3) Kodi Mulungu anasintha bwanji ubale wawo ndi Iye? Kodi kusinthika kwa ubale ku-

meneku kunali kotani? (vv.20, 22)

4) Kodi Akolose anayenera kukhala bwanji mu ubale wawo watsopanowu? (v.23)

Page 17: Colossians bible studies chichewa

17

Tiyeni timvetse zimene ndimeyi ikutanthauza:

5) Onani pa m’ndandanda umene munapanga poyamba zakuti Yesu ndi ndani ndipo

watipangira chiyani ife. Kodi mukuganiza kuti Iye ndi wofunikira ku chikhulupiriro

chathu chifukwa chiyani? Kodi chikumupangitsa Iye kukhala wosiyana ndi atsogoleri

ena a mipingo ndi chiyani?

6) Paulo akunena kuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo chifukwa cha

Iye (v.16). Kodi chilungamo ichi ndi chofunikira bwanji kwa ife potengera cholinga cha

moyo wathu?

Tiyeni tigwiritse ntchito ndimeyi:

7) Kodi mumapeza kuti cholinga cha pa moyo wanu? Chifukwa chiyani?

8) Kodi mwalowa mu ubale watsopano ndi Mulungu? Kodi pali kusintha kwanji m’moyo

wanu pa kukhala mu ubale watsopano ndi Mulungu? (vv. 21-23)

9) Kuti mukule komanso kubala chipatso mu moyo wanu wa chikhristu, Paulo akuti

muyenera kupitirira mu chikhulupiriro, kukhazikika ndi kusasunthika, osachoka pa

chiyembekezo cha Uthenga Wabwino womwe mudamva (v.23). Kodi ndi zinthu zina

ziti zimene zingasunthire chikhulupiriro chanu kutali ndi Yesu?

Kumbukirani Yesu ndi ndani! Iye ndi wamkulu kuposa zonse zimene zimayesa kukunyen-

gererani kuti musaike chikhulupiriro mwa iye.

Page 18: Colossians bible studies chichewa

18

Phunziro mu nkhani yochitika:

Chimwemwe wakhala ali mkhristu kwa zaka zambiri koma anayamba kudziwerengera bai-

bulo yekha posachedwapa. Anapeza Baibulo ngati mphoto ku mbindikiro wa achinyamata

(Youth camp) komwe anapita chaka chatha. Masiku apitawo, anthu awiri ochokera ku mipin-

go ina kumunsi kwa mseu wakwawo anabwera kudzamuyendera ndipo anayamba kumulank-

hula za Yesu pogwiritsa ntchito Baibulo lawo. Koma Chimwemwe anawona kuti Baibulo li-

mene anthu awa amagwiritsa ntchito linali losiyana ndi limene iye anali nalo ndipo linalibe

chizindikiro cha “Bible Society of Malawi”.

Anthuwa anayesa kumuuza Chimwemwe kuti Yesu si Mulungu koma analengedwa ndi

Mulungu ngati “mwana woyamba” pa chilengedwe chonse. Chimwemwe akudziwa mumtima

mwake kuti izi sizolondola koma sakudziwa kayankhidwe kake. Mozunguzika, anabwera kwa

inu kuti mumuthandize chifukwa akudziwa kuti mwakhala mukuphunzira za Yesu mu buku la

Akolose. Kodi mumulangiza bwanji kuchokera mu ndime ya Akolose imene mwaphunzira

lero? (Mukhoza kuwonanso Yohane 1:1-3; Afilipo 2:6)

Mfundo yaikulu mu phunziro:

Yesu ndi maziko a chikhulupiriro chathu. Iye ndi munthu wofunikira kwambiri kumudziwa pa

dziko lonse chifukwa Iye ndiye Mulungu. Iye ndi yekhayo amene akanatiwombola ndi kuti-

yanjanitsa ndi Mulungu. Ichi ndi chimene chimasiyanitsa chikhristu ndi zipembedzo zina.

Zipembedzo zina zimanena kuti kuli njira zambiri zopitira kwa Mulungu. Chikhristu

chimanena kuti Yesu ndi njira yokhayo yopitira kwa Mulungu. Chifukwa Mulungu anatilenga

ndipo anatipulumutsa, ife ndife ake ndipo amatipatsa cholinga chathu chatsopano cha moyo.

Kuti tikule ndi kubala chipatso mu moyo wathu wa chikhristu, tiyenera kumudziwa Yesu

bwino ndi kumulola kuti alamulire chilichonse pa moyo wathu.

Tiyeni tipemphere:

Yambani nthawi yanu yopemphera polemekeza Yesu pa zonse zimene mwaphunzira za Iye,

ndiponso chifukwa cha zonse zimene wakuchitirani. Mupempheni Mulungu akuthandizeni

kukula pa kamvetsedwe kanu ka Yesu ndiponso kuyika moyo wanu mu dongosolo ndi zolinga

za Mulungu kuti muthe kukhala moyo watanthauzo umene uli womukondweretsa Iye.

Page 19: Colossians bible studies chichewa

19

Phunziro 3 – Kodi timakula bwanji mu moyo wathu wa uzimu?

Ndime yophunzira ya m’Baibulo: Akolose 1:24-2:5

Mau oyamba a phunziro:

Mu ndimeyi, Paulo akupitiriza pamene anasiyira pa vesi 23. Akunena za iye mwini pokhala

mtumiki wa Uthenga Wabwino umene unalalikidwa mu chilengedwe chonse (v23). Paulo

akulankhula za masautso ndi mavuto ake mu cholinga chodziwitsa “chinsinsi” cha Uthenga

Wabwino ndi kuonetsera aliyense wokhwima mwa Khristu. Ndi chinsinsi chimenechi

chimene chinakhala poyambira pa mphamvu ndi kukula pa moyo ndi mu utumiki wake.

Chinsinsichi chingatithandizenso pa kukula kwa moyo wathu wauzimu.

Tiyeni ticheze:

Kodi liu loti “Chinsinsi” limatanthauza chiyani ? Kodi mumadziwa za “Chinsinsi” china

chake?

Nanga chinsinsi chimene Paulo akunena ndi cha mtundu uwu? Kapena anali ndi tanthauzo

lina m’maganizo ake? Tiyeni tifufuze mu ndime ya mu Baibulo ndipo tipeze!

Tiyeni tiwone zimene ndimeyi ikunena:

1) Kodi Paulo akuzunzikira chiyani? Nanga maganizo ake ndi otani pa mazunzowo?

(vv.24-25)

2) Kodi ndi chinsinsi chotani chimene Paulo akuchifotokozachi? (vv. 26-27; 2:2-3)

3) Kodi Paulo akulakalaka kuona chiyani chikuwachitikira Akolose? (1:28; 2:2-5)

Page 20: Colossians bible studies chichewa

20

Tiyeni timvetse zimene ndimeyi ikutanthauza:

4) Paulo anatanthauzira liu la “Chinsinsi” ngati “Khristu mwa inu, chiyembekezo cha

ulemerero” (v.27). Kudziwa kuti ali ndi Khristu mwa iye komanso chiyembekezo cha

ulemerero, ndi chifukwa chiyani izi zikanamuthandiza kudutsa mu masautso ndi

m’mavuto pa moyo ndi utumiki wake (v29)?

5) Chifukwa chiyani Paulo akufuna kuti Akolose adziwe chinsinsichi? (vv2:2-4)

Tiyeni tigwiritse ntchito ndimeyi:

6) Kodi mukumudziwa Yesu pa nokha ndi chiyembekezo cha ulemerero chimene amaku-

patsani? Kambiranani ndi anzanu umboni wanu wa m’mene “Khristu mwa inu -

chiyembekezo cha ulemerero” akuthandizirani mu nyengo za masautso ndi mavuto

anu.

7) Paulo akuyesetsa kuti apereke anthu okhwima mwa Yesu pofalitsa Uthenga, kuchen-

jeza ndi kuwaphunzitsa ndi nzeru zonse, ndipo kupanga izi mwa mphamvu ya Khristu

imene imagwira ntchito mwamphamvu mwa Iye. Paulo anamvetsa kuti chiyambi cha

kukula mu chikhristu ndi Yesu. Kodi tingathandize bwanji ena kukhwima mu moyo wa

chikhristu?

8) Paulo anali wokonzeka kuzunzika chifukwa cha anthu ena amene sanakumanepo

nawo pamaso ndi pamaso (2:1) ndi cholinga chakuti amudziwe Yesu ndiponso kukula

mwa Iye. Kodi ndinu okonzeka kudzipereka kupirira kudutsa mu zokhoma chifukwa

cha anthu ena amene simukuwadziwa kuti mwina iwo angamudziwe Yesu? Kodi ndi

zokhoma zotani zimene mungakumane nazo poyesa kuthandiza anthuwa kumudziwa

Yesu? Kodi chitsanzo cha Paulo chingakuthandizeni bwanji kuthana ndi zokhomazo?

Page 21: Colossians bible studies chichewa

21

Phunziro mu nkhani yochitika:

Yohane wakhala ali membala mu gulu la achinyamata kwa nthawi yaitali. Amapita ku

tchalitchi masabata ambiri koma akumva kuti sakukula ngati mkhristu. Amapita ku mis-

onkhano ya chikhristu yachitsitsimutso kumene kumatsindika za machiritso komanso kukha-

la anthu olemera. Iye amamvetseranso kwambiri za olalikira a pawailesi amene amauza an-

thu kuti ayenera kupereka ndalama ku utumiki wawo kuti Mulungu awadalitse ndi mphamvu

zokula mu uzimu ndi kuchita bwino mu chaka chomwecho. Iye amakhumbira kukula mu uzi-

mu choncho amapereka ndalama zake zonse zimene amapeza ku ganyu ku misonkhano ya

chitsitsimutso kumene amapitako. Ngakhale wakhala akuchita izi, iye akumvabe kuti zinthu

sizinasinthe. Amakhumudwa chifukwa iyeyu akukhulupirira mu zochitika za m’chipembedzo,

ndi mu njira za m’chipembedzo kuti zimuthandiza kukula. Choncho, Kuchokera ku zimene

mwaphunzira lero mu Akolose, Kodi mungamulangize bwanji Yohane pa m’mene angakulire

mu uzimu woonadi?

Mfundo yaikulu mu phunziro:

Yesu Khristu ndi chinsinsi chimene chakhala chobisika ndi Mulungu kwa nthawi yaitali, koma

tsopano chavumbulutsidwa ndi Mulungu kudzera mu Uthenga Wabwino. Pakuti ife amene

tinalandira Khristu, tili ndi chuma ndi chiyembekezo cha ulemerero mkati mwathu. Yesu ndi

chiyambi cha kukula kwathu mu uzimu, ndipo amatipatsa kuthekera kopirira m’masautso ndi

m’zokhoma chifukwa cha ena kuti nawonso adziwe za chuma chimenechi. Osapita kwina kuti

mukule mu uzimu. M’malo mwake pitani kwa mwini moyo weniweni, amene ali chuma ndi

chiyembekezo chathu, Yesu Khristu Ambuye wathu. Chiyembekezo chathu ndi chimwemwe

chathu chagona pa choonadi monga zinavumbulutsidwa kwa ife mu Baibulo, osati pa-

zakumva, kapena zochitika zozizwitsa.

Tiyeni tipemphere:

Lemekezani Mulungu chifukwa anativumbulutsira Yesu Khristu kudzera mu Uthenga

Wabwino kuti tikadziwe chipulumutso ndi moyo umene amapereka. Tipemphere kuti tithe

kudalira pa Yesu ngati chiyambi chenicheni cha kukula kwathu mu uzimu osati zabodza zinazi

zimene zimadalira nzeru ndi njira za anthu. Pempherani kuti mukathe kupirira m’masautso

ndi m’zokhoma kuti anthu ena akadziwe za chuma chimene muli nacho mwa Yesu.

Page 22: Colossians bible studies chichewa

22

Phunziro 4 – Osanamizidwa ndi m’mene dziko la pansi limaganizira

Ndime yophunzira ya m’Baibulo: Akolose 2:6-23

Mau oyamba a phunziro:

Taganizirani kugula feteleza wotsika mtengo amene sali feteleza weniweni kenaka inu

ndikudzamuzindikira pamene mbeu zanu sizinabale zipatso pa nyengo yokolola.

Chimodzimodzinso tikalephera kudyetsera miyoyo yathu ya chikhristu ndi Yesu, ndi kumaten-

geka ndi zina zofanana ndi Yesu, tidzalephera kubala zipatso kapenanso tidzaferatu ku uzimu.

Mu ndime ya lero, Paulo akutichenjeza za kuopsa kwa ziphunzitso za bodza zimene zim-

akankhira chikhulupiriro chathu kutali ndi Yesu.

Tiyeni ticheze:

Kodi zinthu zina zimene zingasokoneze chimanga kuti chikule bwino ndi ziti?

Tiyeni tiwone zimene ndimeyi ikunena:

1) Kodi Paulo akuwauza Akolose kuti achite chiyani? (vv. 6-7)

2) Kodi Paulo akuwachenjeza Akolose za chiyani? (v. 8)

3) Kodi Paulo akuwakumbutsa Akolose za Yesu kuti ndi ndani ndipo wawachitira chi-

yani? (vv. 9-15)

4) Malingana ndi Paulo, kodi munthu amadzichotsa bwanji yekha kukhala m’moyo

wathunthu mwa Yesu? (vv. 18-19)

Page 23: Colossians bible studies chichewa

23

Tiyeni timvetse zimene ndimeyi ikutanthauza:

5) Chifukwa chiyani kukula kwathu ngati akhristu kumatsamira pa chikhulupiriro mwa

Yesu osati pongoyang’ana ziphunzitso za anthu, malamulo ndi zikhalidwe? (Onani

vesi 9 ndi 19)

6) Kodi ndi chifukwa chiyani ziphunzitso za anthu zokha sizingatiletse kugwa

m’mayesero a thupi? (v23)

Tiyeni tigwiritse ntchito ndimeyi:

7) Kodi malamulo ndi chikhalidwe cha mpingo zingakhale zosathandiza bwanji mu moyo

wanu wa chikhristu? Kodi zingathandize bwanji? Kodi mungakhale bwanji okhazikika

ndi okula mwa Khristu?

8) Kodi ziphunzitso zina zabodza zimene munamvapo kwa anthu ndi ziti? Kodi mukudzi-

wa bwanji kuti ndi zonama? Nanga mungapewe bwanji kuti musanamizidwe ndi

ziphunzitso za bodzazi?

Page 24: Colossians bible studies chichewa

24

Phunziro mu nkhani yochitika:

Tiyamike wakhala mkhristu posachedwapa. Tsiku lina analandira alendo awiri kunyumba

kwake amene anamuphunzitsa kuti kukhala Mkhristu weniweni, ayenera kulowa mpingo

wawo, kusala kudya katatu pa sabata ndipo kumatha kuwona angelo m’masomphenya ko-

manso kukhala ndi zochitika za mphamvu ya uzimu monga kulankhula m’malilime

(mchilankhulo cha kumwamba). Atachoka alendowo, Tiyamike wazunguzika ngati iye ali

mkhristu weniweni kapena ayi. Kodi atabwera kwa inu mungamulangize bwanji?

Mfundo yaikulu ya mu phunziro

Munawoloka kuchokera ku imfa kupita ku moyo pamene munalandira Yesu ngati Ambuye

wanu. Choncho pitirizani kukhulupirira Iye kuti mukule mu uzimu. Musakhale akapolo a

ziphunzitso zabodza kapena zochitika ndi malamulo a zipembedzo zimene zingakulepheret-

seni kukhulupirira Yesu. Ndi kosavuta kunamizidwa ndi dziko lapansi makamaka ngati ife

sitikudziwa zomwe baibulo likuphunzitsa. Ndikofunikira kwambiri kudziwa baibulo lanu kuti

muthe kupanga chisankho pa nokha kuti ichi ndi choona kapena ayi. Mukadziwa choonadi,

choonadicho chidzakumasulani. Chidzakumasulani ku mantha, kusokonezeka, komanso

nkhawa yokhudza kupeza chipulumutso mu mphamvu zanu. Mverani mau a Mulungu

m’malo momvera mau a athu ambiri a ku dziko lapansi. Chipulumutso chanu chimapezeka

champhumphu mwa Khristu yekha.

Tiyeni tipemphere:

Thokozani chifukwa mwapangidwa kukhala a moyo mwa Yesu. Mupempheni Mulungu aku-

thandizeni kukhala okhazikika mwa Yesu pa kukula kwanu ndiponso osadalira zinthu zina.

Mupempheni Mulungu akupatseni nzeru ndi kutha kusiyanitsa ziphunzitso zoona za mu Bai-

bulo ku ziphunzitso zonama kuti moyo wanu upeze chonde ndi chakudya choyenera cha

uzimu chimene mungakule nacho.

Page 25: Colossians bible studies chichewa

25

Phunziro 5 – Moyo wosinthika

Ndime yophunzira ya m’Baibulo: Akolose 3:1-17

Mau oyamba a phunziro:

Pamene tinalandira Yesu ngati Ambuye wa moyo wathu, tinayamba moyo watsopano mwa

Iye. Tidzakhala tikuyenda mwa Iye Ozika mizu ndi omangiririka mwa Iye (2:6) ngati m’mene

mtumiki Paulo anatikumbutsira mu phunziro latha. Koma moyo watsopanowu umaoneka

bwanji pofanizira ndi wakale umene tinkayendamo? Tiyeni tiphunzire ndime ya lero ya mu

Baibulo kuti tizipeze izi.

Tiyeni ticheze:

Kodi mukuvomereza kapena mukutsutsana ndi zonenedwa izi: “Zimene mumavala

zimafotokoza za m’mene inu mulili.” Chifukwa chiyani?

Tiyeni tiwone zimene ndimeyi ikunena:

1) Kodi ndi makhalidwe a “moyo wakale” ati amene Paulo akunena kuti tiyenera

“kuwapha?” (vv. 5-10)

2) Kodi ndi makhalidwe a “moyo watsopano” ati mwa Khristu amene Paulo akunena kuti

tiyenera kuwavala?” (vv. 12-17)

3) Chifukwa chiyani Paulo akuwauza Akolose kuti “aphe” moyo wakale ndipo “avale”

moyo watsopano? (vv. 1- 4)

4) Kodi Paulo akutipatsa kuzindikira kwina kotani pa za moyo wathu “watsopano” mu

vesi 10-11?

Page 26: Colossians bible studies chichewa

26

Tiyeni timvetse zimene ndimeyi ikutanthauza:

5) Kodi “mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu” (v.1) kumatanthauza chiyani? Ndipo

“moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu” (v.3) kuma-

tanthauza chiyani? Fanizirani ndi zimene Paulo ananena kumayambiriro mu Akolose

2:13-14.

6) “Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu” (v. 15) kumatanthauza

chiyani? Ndipo siyani “Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu” (v.16)

akutantauza chiyani?

Tiyeni tigwiritse ntchito ndimeyi:

7) Kodi ndi makhalidwe ati a “moyo wakale” amene mukuganiza kuti ndi ovuta

“kuwapha” ndipo ndi makhalidwe ati “amoyo watsopano” amene ndi “ovuta” kwam-

biri “kuwavala”? Chifukwa chiyani?

8) Kodi ndi phindu lanji ndipo ubwino wanji umene mumauona pokhala “m’moyo

watsopano” umene ndi “woyang’ana ena” kuposa wakale “woziyang’ana wekha”

Page 27: Colossians bible studies chichewa

27

Phunziro mu nkhani yochitika:

Yamikani ndi membala wagulu la achinyamata ku mpingo, ndipo makolo ake ndi Madikoni

olimbikira ku tchalitchi .Ngakhale Yamikani amadziwonetsera kuti ndi M’khristu ndipo amapi-

ta ku tchalitchi la Mulungu, koma khalidwe lake mkati mwa sabata limaonetsera zina zake.

Amagonana ndi chibwenzi chake, amaledzera ndipo amakwiya msanga.Yamikani ama-

khulupirira kuti kupita ku tchalitchi ndi kumene kumamupangitsa iye kukhala mkhristu ndipo

kumafuta zinthu zonse zoipa zimene amachita. Kodi mungamufotokozere bwanji kuchokera

ndime imene tawerenga lero za tathauzo lokhala M’khristu.

Mfundo yaikulu mu phunziro:

Yesu anakuferani kuti mukhale ndi moyo watsopano. Pamene mwalandira moyo watsopano

mwa Khristu, simuchitanso zinthu zodzikondweretsa nokha, koma zokondweretsa Mulungu

komanso anthu ena.

Tiyeni tipemphere:

Mutamandeni Mulungu chifukwa cha moyo watsopano umene wakupatsani mwa khristu.

Mupempheni Mulungu akuthandizeni kuyenda mu moyo watsopanowu ndi kubala chipatso

m’menemo. Pempherani kuti Mulungu akutetezereni komanso ena a mu gulu lanu la

achinyamata kuti musabwerere m’mbuyo ku njira zakale zimene zimatitengera ku imfa.

Page 28: Colossians bible studies chichewa

28

Phunziro 6 – Ubale wosinthika

Ndime yophunzira ya m’Baibulo: Akolose 3:18-4:1

Mau oyamba a phunziro:

Muphunziro lathu latha, tinaphunzira za kuyenda mu moyo watsopano ndi Yesu osati kuyen-

da mu moyo wathu wakale umene ndi wa uchimo. Mu mutu 3 ndime 17, Paulo akunena kuti

“Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite

m'dzina la Ambuye Yesu...” Mu ndime ya lero, tiwona tanthauzo la ndime iyi potengera ubale

wa anthu wa tsiku ndi tsiku, ndipo tanthauzo la kubala chipatso mu maubale amenewa

kuwonetsera Yesu amene ali mwa nu.

Tiyeni ticheze:

Ngati gulu, pezani limodzi ma ubale osiyanasiyana amene amapezeka mudziko.

Kodi chifukwa chiyani ma ubale ndiwofunikira?

Tiyeni tiwone zimene ndimeyi ikunena:

1) Kodi ndi ubale wa anthu uti wa tsiku ndi tsiku umene Paulo akunena mu ndime iyi?

2) Kodi Paulo akuphunzitsa mtundu uliwonse kuchita chiyani?

Tiyeni timvetse zimene ndimeyi ikutanthauza:

3) Chifukwa chiyani “kudzipereka” ndi “chikondi” ndi zofunikira kwambiri pa ubale wa

m’banja? Kodi ziwirizi zimathandizira bwanji? (vv.18-19)

Page 29: Colossians bible studies chichewa

29

4) Chifukwa chiyani ndi zofunika kuti ana ndi achinyamata adzimvera makolo awo? Ma-

kolo angachite chiyani kuthandiza ana awo ndi achinyamata kumvera mosangalala

osati mokakamizika? (vv.20-21)

5) Chifukwa chiyani ndizofunika kukhala ndi maganizo abwino pa ntchito yanu ndiponso

anthu amene mumawagwirira ntchito? (vv. 22-24)

Tiyeni tigwiritse ntchito ndimeyi:

6) Kodi ndimeyi tingayigwiritse ntchito bwanji mu izi:

Ubale wa m’banja (ndi makolo kapena abale ena)

Ubale wa pa chibwenzi kapena ukwati

Ubale wa pa ntchito

Opemphera nawo.

Anthu ena

7) Kodi moyo wathu watsopano ungatithandize bwanji kukhala bwino m’maubale ame-

ne tilimo? Onaninso makhalidwe “atsopano a iwe wekha” amene tili nawo mwa

khristu (3:12-17)

8) Kodi mukuganiza kuti chingachitike ndi chiyani m’madera mwathu ngati aliyense wa

ku tchalitchi kwanu angakhale pa ubale ndi anthu akunja kwa tchalitchi mu njira

imene imaonetsa Yesu amene ali mwa inu?

Page 30: Colossians bible studies chichewa

30

Phunziro mu nkhani yochitika:

Mphatso ndi membala wagulu la achinyamata. Iye amanena kuti ndi mkhristu koma akuvuti-

ka kuti akule mu moyo wake wa uzimu. Akumva kuti sakusintha mu ulendo wake wa uzimu

kuyambira tsiku limene analandira khristu m’moyo wake. Nkhani ndiyakuti, iye ali ndi vuto

ndi maubale a tsiku ndi tsiku. Iye samakonda kumvera makolo ake ndipo kawirikawiri amachi-

ta zotsephana ndi zimene amamuuza, iyeyo akuziona kuti wakula angachite zinthu munjira

yake. Alinso ndi vuto ndi abwana ake ku ntchito amene amawada kwambiri. Amagwira ntchi-

to pokhapokha abwanawo akakhalapo koma akangochoka, iye amangokhala nkumacheza ndi

anzake. Kutchalitchi samalabadira kwambiri za anzake a mugulu lachinyamata, amalakhula

mwamwano kwa anthu aakulu aku tchalitchi. Kodi mungamupatse malangizo otani oti

amuthandize kuyamba kukula mu moyo wa chikhristu?

Mfundo yaikulu mu phunziro:

Ngati muli ndi khristu mwa inu, zidziwonekera mu maubale anu ndi anthu. Ubale wanu uy-

enera kukhala wofanana ndi moyo wanu mwa khristu osati moyo wanu wakale wa uchimo.

Moyo wosinthika umabweretsa ubale wosithika. Sindifenso “odziona tokha” ndipo tifunefune

kupeza chimene tingachite kwa ena. M’malo mwake tsopano ndife “oona za ena” ndipo

tifunefune kuwonetsera kwa ena Yesu amene amakonda chilungamo, wachisoni ndi wachi-

fundo.

Tiyeni tipemphere:

Mutamandeni Mulungu chifukwa cha anthu onse amene wawaika mu moyo wanu. Mupem-

pheni Iye kukuthandizani kuwonetsera Yesu kwa iwo, osati uchimo wanu wakale. Mupem-

pheni iye kubweretsa kusintha kwabwino mu maubale anu ndi anthu a mu banja lanu,

kutchalitchi ndi kumadera kwanu kuti dzina la Yesu likalemekezedwe.

Page 31: Colossians bible studies chichewa

31

Phunziro 7- Cholinga Chatsopano

Ndime yophunzira ya m’Baibulo: Akolose 4:2-18

Mau oyamba a phunziro:

Mathero a bukhu lili lonse kapena filimu amabweretsa zonse zimene zinalembedwa kapena

zawonetsedwa poyamba. Chimodzimodzi mu kalata ya Paulo kwa Akolose, akumaliza ndi

mau awa, “Kumbukirani kuti ndili m'maunyolo” (4:18). Mukuwona, Paulo anali mu ndende

pamene amalemba kalata iyi, ndipo anali mu ndende chifukwa cha Uthenga Wabwino. Kud-

ziwitsa Yesu kwa ena kudzera mu Uthenga Wabwino. Kudziwitsa Yesu kwa ena kudzera mu

Uthenga Wabwino chinali cholinga chatsopano cha moyo wa Paulo. Uthenga Wabwino wa

Yesu unali waukulu kwambiri moti ukanamupititsa iye ku ndende. “unyolo wake” ukulank-

hula kufunikira kwa Uthenga Wabwino! Ukubweretsa zonse zimene ananena mu Kalata yake

poyera - kuti Uthenga Wabwino ndi wofunikira kwambiri motero samayenera kuunyalanyaza

kapena kuuika m’malo mwa uthenga wabodza.

Choncho tiyeni tiwonetsetse gawo lomaliza la kalata ya Paulo ndiponso malangizo omaliza

amene wapereka kwa Akolose. Zinthu zitatu zatulukira mu gawo limeneli zimene ndi zo-

funikira chidwi chathu: (1) Pemphero; (2) Zochitika zoima pa Uthenga Wabwino; (3) Kugwir-

ira ntchito pamodzi.

Tiyeni ticheze:

Mukanakhala kuti mukulembera kalata mu ndende yopita kwa okondedwa anu, kodi

mukanamaliza bwanji kalata yanuyo? Mau omaliza akanakhala otani?

Tiyeni tiwone zimene ndimeyi ikunena:

1) Kodi Paulo akuwauza Akolose chiyani za m’mene adzipempherera mu vesi 2-4?

2) Kodi Paulo akuwauza Akolose chiyani za m’mene adzikhalira ndi anthu osakhulupiri-

ra? (vv..5-6)

3) Paulo akumaliza kalata yake ndi moni kuchokera kwa anzake ogwira nawo ntchito mu

vesi 7-18. Lembani ndandanda wa anzake ogwira nawo ntchito ndiponso m’mene

Paulo anawafotokozera .

Page 32: Colossians bible studies chichewa

32

Tiyeni timvetse zimene ndimeyi ikutanthauza:

4) Kodi zikutanthauza chiyani “Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene

mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu”? (v. 2)

5) Kodi mau awa akutanthauzira chiyani kwa ife: (1) kuyenda mu nzeru kufikira akunja

kugwiritsa ntchito bwino nthawi (2) kuti zolankhula zathu zikhale “zachisomo” ndi

“zothiridwa mchere?” Kodi izi ndi zofunikira bwanji pamene tikupanga ubale ndi

osakhulupirira? (vv.5 -6)

6) Kodi tingaphunzirepo chiyani pa za ubale wa Paulo ndi anzake ogwira nawo ntchito

mu Uthenga Wabwino? Ndipo kodi izi ndi zofunikira bwanji ngati tikufuna kubala

zipatso mu utumiki wathu?

Page 33: Colossians bible studies chichewa

33

Tiyeni tigwiritse ntchito ndimeyi:

7) Epafirasi anali m’modzi mwa ogwira ntchito ndi Paulo amene Paulo akumufotokoza

kuti amavutika m’malo mwa Akolose m’mapemphero ake kuti mwina Akolose an-

gaime mozama ndi kukhala ndi chitsimikizo mu chifuniro chonse cha Mulungu. Lem-

bani ndandanda wa anthu m’moyo ndi mu utumiki wanu amene mungama-

wapempherere pafupipafupi mu njira imeneyi.

8) Kodi ndi mbali iti ya moyo wanu ndi zolankhula zanu zimene muyenera kusintha kuti

mukope osakhulupirira ku chikhulupiriro mwa Yesu?

9) Malangizo omaliza a Paulo kwa ogwira naye ntchito Archipasi ndi akuti, “Ona kuti

ukwaniritse utumiki umene walandira mwa Ambuye” (v 17) Kodi ndi utumiki uti

umene mwalandira kwa Ambuye umene mukuyenera kuukwaniritsa? Kodi chiku-

kubwezerani kumbuyo mu utumiki umenewu ndi chiyani? Pempherani ndi kumupem-

pha Mulungu akuthandizeni kukhala obala zipatso mu utumikimo, ndi kukhala,

“tcheru” m’mene Iye ayankhire mapemphero anu.

Page 34: Colossians bible studies chichewa

34

Phunziro mu nkhani yochitika:

Precious ndi mtsikana, membala wagulu lake la achinyamata ndipo wafunsidwa ndi abusa ake

kukonzekeretsa gulu lake la achinyamata kufikira anthu ndi kuchita chitsitsimutso ku mudzi

wina wapafupi. Iye akuvutika kupeza mfundo zoti akaphunzitse a gulu lake la achinyamata za

m’mene angachitire chitsitsimutso. Iye abwera kwa inu kudzafunsa thandizo. Kodi mumulan-

giza bwanji zimene angakaphunzitse kuchokera mu bukhu la Akolose:

Uthenga Wabwino (onani 1:13-23)

Njira imene angapangire chitsitsimutso. (onani 4: 2-6)

Mfundo yaikulu mu phunziro:

Uthenga Wabwino umatipatsa cholinga chatsopano m’moyo, chimene chimadziwitsa Yesu

kwa ena kudzera m’mau ndi m’zochitika. Tiyenera kupemphera, kuwonetsa kudalira kwathu

pa Mulungu. Tiyenera kukhala ndi khalidwe labwino ndiponso tiyenera kulankhula mu njira

imene imapangitsa chikhulupiriro chathu kukhala chachikoka kwa osakhulupirira. Tiyenera

kudzipereka kugwira ntchito pamodzi ndi anzathu okhulupirira, mu umodzi osati mwa

mpikisano, kuti tifalitse Uthenga Wabwino wa Yesu.

Tiyeni tipemphere:

Muyamikeni Mulungu chifukwa cha utumiki umene wakuitanirani kuti muuchite, palibe kan-

thu kuti ndi waung’ono bwanji. Mupempheni Mulungu akuthandizeni kubala zipatso mu

utumiki uwu, ndipo kuti udzaonetsere Yesu kwa osakhulupirira ndiponso kwa onse amene

Mulungu waitana kugwira ntchito pamodzi ndi inu.

Page 35: Colossians bible studies chichewa

35

Page 36: Colossians bible studies chichewa

36

Maphunziro asanu ndi awiri (7) mu kabuku:

Phunziro 1 Uthenga Wabwino ndi chiyani?

Phunziro 2 Kodi Yesu ndi wofunikira chifukwa chiyani?

Phunziro 3 Kodi timakula bwanji mu moyo wathu wa uzimu?

Phunziro 4 Osanamizidwa ndi m’mene dziko lapansi limaganizira!

Phunziro 5 Moyo wosinthika

Phunziro 6 Ubale wosinthika

Phunziro 7 Cholinga chatsopano