28
OPA NDA NDALAMA KA PENA OPA NDA MTENGO Ndithudi ndi chamwayi kubwerera ku kachisi, mmawa uno. Ine ndikungodabwa…M’bale Neville ananena kuti ambiri samatha kumva kumbuyoko. Mukundimva ine bwino lomwe tsopano, kumbuyo uko? Kodi zonse ziri bwino? Chabwino. Ndine—ndine wamng’ono, chotero ndimayenera kupanga phokoso lambiri kuti anthu adziwe kuti ndiripo. 2 Chotero, ine ndikukumbukira nthawi ina pamene ine ndinkagwira ntchito Kolipirira Mabilu. Ine ndikamakwera pa sitepe…Ndipo ine ndinkakonda kuvala nsapato zazikulu kwambiri, zokhala ndi gogoda pa izo, kuchokera koyendera nthambo za m’mwamba. Ndipo ine ndinkabwera chokwera masitepe. Ndipo Akazi a Ehalt, yemwe ali mzanga wa ine, amakhala pa switchibodi. Ine ndikutsimikiza Bambo Ginther kumeneko akhoza kumuzindikira iye, bwino lomwe. Chotero Edith anati, “Billy, iwe umapanga phokoso lowonjeza, losagwirizana ndi munthu wamng’ono, yemwe ine ndinayamba ndamuwonapo.” Ndikuponda magogoda awa aakulu, ndikukwera pamwamba pa masitepe. 3 Ine ndinati, “Chabwino, Edith, ndine wamng’ono kwambiri, ine ndiyenera kuyesetsa kuti aliyense adziwe kuti ine ndiripo, pomapanga phokoso lambiri.” 4 Chabwino, ine ndinangopita mkati kuti ndikaimbe. M’bale Neville anali atandiuza ine kuti bwenzi lathu labwino, M’bale Roy Roberson, monga ali kutali ndi msonkhano mmawa uno, pa chifukwa chakuti akudwala. Lake…Iye wakhala ali ndi dzino lophatana. Ilo layambitsa matenda, ndipo zikumpatsa iye kutentha thupi. Ndipo iye ndiwoti akalizulitse ilo, ine ndikuganiza, pomwepo. Ndipo Roy wakhala ali ngati bambo kwa ife kuno, ndipo ife timamukonda iye. Ndipo ine ndinati, “M’bale Roy, ine—ine ndikukalowa tsopano, mu maminiti pang’ono chabe, mu msonkhano.” Ine ndinati, “Ine ndikaupempha mpingo kuti ife tonse tikupempherere iwe, mmawa uno,” ndipo mawa pamene iye azidzapita uko, kuti akasamalire izi. Dzinolo latuluka mopingasa, kapena chinachake, laphatirira molakwika, ndipo iwo akuyenera kuti akalidulepo ilo, ndi kulichotsapo. 5 M’bale Roy ndi wa nkhondo wakale, monga inu nonse mukudziwa, kuchokera ku Nkhondo Yachiwiri ya Dziko lonse, yemwe anawomberedwa m’zidutswa. Ndipo kukanakhala kuti si kwa ubwino wa Mulungu, iye sibwenzi ali moyo nkomwe.

CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

  • Upload
    others

  • View
    2

  • Download
    0

Embed Size (px)

Citation preview

Page 1: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA

OPANDA MTENGO

Ndithudi ndi chamwayi kubwerera ku kachisi, mmawa uno.Ine ndikungodabwa…M’bale Neville ananena kuti ambiri

samatha kumva kumbuyoko. Mukundimva ine bwino lomwetsopano, kumbuyo uko? Kodi zonse ziri bwino? Chabwino.Ndine—ndine wamng’ono, chotero ndimayenera kupangaphokoso lambiri kuti anthu adziwe kuti ndiripo.2 Chotero, ine ndikukumbukira nthawi ina pamene inendinkagwira ntchito Kolipirira Mabilu. Ine ndikamakwerapa sitepe…Ndipo ine ndinkakonda kuvala nsapato zazikulukwambiri, zokhala ndi gogoda pa izo, kuchokera koyenderanthambo za m’mwamba. Ndipo ine ndinkabwera chokweramasitepe. Ndipo Akazi a Ehalt, yemwe ali mzanga waine, amakhala pa switchibodi. Ine ndikutsimikiza BamboGinther kumeneko akhoza kumuzindikira iye, bwinolomwe. Chotero Edith anati, “Billy, iwe umapanga phokosolowonjeza, losagwirizana ndi munthu wamng’ono, yemweine ndinayamba ndamuwonapo.” Ndikuponda magogoda awaaakulu, ndikukwera pamwamba pamasitepe.3 Ine ndinati, “Chabwino, Edith, ndine wamng’ono kwambiri,ine ndiyenera kuyesetsa kuti aliyense adziwe kuti ine ndiripo,pomapanga phokoso lambiri.”4 Chabwino, ine ndinangopita mkati kuti ndikaimbe. M’baleNeville anali atandiuza ine kuti bwenzi lathu labwino, M’baleRoy Roberson, monga ali kutali ndi msonkhano mmawauno, pa chifukwa chakuti akudwala. Lake…Iye wakhalaali ndi dzino lophatana. Ilo layambitsa matenda, ndipozikumpatsa iye kutentha thupi. Ndipo iye ndiwoti akalizulitseilo, ine ndikuganiza, pomwepo. Ndipo Roy wakhala ali ngatibambo kwa ife kuno, ndipo ife timamukonda iye. Ndipoine ndinati, “M’bale Roy, ine—ine ndikukalowa tsopano,mu maminiti pang’ono chabe, mu msonkhano.” Ine ndinati,“Ine ndikaupempha mpingo kuti ife tonse tikupempherereiwe, mmawa uno,” ndipo mawa pamene iye azidzapita uko,kuti akasamalire izi. Dzinolo latuluka mopingasa, kapenachinachake, laphatirira molakwika, ndipo iwo akuyenera kutiakalidulepo ilo, ndi kulichotsapo.5 M’bale Roy ndi wa nkhondo wakale, monga inu nonsemukudziwa, kuchokera ku Nkhondo Yachiwiri ya Dziko lonse,yemwe anawomberedwa m’zidutswa. Ndipo kukanakhala kutisi kwa ubwino wa Mulungu, iye sibwenzi ali moyo nkomwe.

Page 2: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

2 MAWU OLANKHULIDWA

Iye anakagonekedwa pamodzi ndi akufa, kwa nthawi yaitali;manja ataomberedwa kuno, ndipo miyendo itaphulitsidwa,ndipo mitsempha yaikulu yonse itaphedwa. Ndipo adokotalaanati, “Ngati iye angakhale moyo konse, iye sadzayenda sitepenkomwe.” Mwa chisomo cha Mulungu, iye amagwira ntchitotsiku lirilonse, kumakwera ndi chirichonse. Mulungu wakhalaali wabwino kwa iye chifukwa iye ndi munthu wabwino, ndipoife timamukonda iye. Ndipo ife, ife tiri—ife sitiri tonse…6 Ife tikamakhala moyo wabwino, izo sizitanthauza kutiife ndiwoti sitingakumane ndi mavuto. Moonamtima, izozimatanthauza kuti mavuto onse alunjikitsidwira njira yathu.“Pakuti zambiri ndi zotunduza za olungama, koma Mulunguamamuwombola iye kwa izo zonse.”Ndiro gawo la ulemelero.7 Chotero ife tingopempha pemphero lapadera mmawa uno,la M’bale Roy. Ine ndikudabwa ngati alipo aliyense muno,pakalipano, akufuna kuti apemphereredwe, akufuna kutiakumbukiridwe mu mawu a pemphero? Ngati iwo angakwezechabe manja awo. Chabwino. Ndizo zabwino. Tiyeni tingoimakwa kamphindi chabe, ngati inu mungatero, pamene ifetikupemphera.8 Ambuye, ife tikubwera lero, pakuyamba kwa sabata. Ndipodzuwa likungotenga njira yake tsopano, kuti liwuluke kudutsapa dziko lapansi, kuti libweretse kuwala ndi moyo kwazinthu izo zimene ilo linakonzedwera kuti lidzachite. Ndipopa kuyamba kwa msonkhano umene…Ife tiri gawo la MpingoWanu, umene wayitanidwa kuti udzachititse misonkhano yamachiritso, machiritso a thupi; kukakwaniritsa zofuna ndizokhumba za Ambuye wathu wodala Yemwe anavulazidwachifukwa cha zolakwa zathu, ndipo ndi mikwingwirima Yakeife tinachiritsidwa. Ndipo ife tikufuna tipemphe, pa kuyambakwa msonkhano, pamene ukuyamba kutenga mapiko ake,mu nyimbo, ndipo mitima yathu ikuyamba kukwezedwam’mwamba, kuti ife tikhoze kukumbukira, mmawa uno,Ambuye, m’bale wathu wokondedwa, wofunika, Roy Roberson,wantchito Wanu wodzichepetsa. Ndipo ife tikudziwa kuti Inumunasunga moyo wake ku bwalo la nkhondo, ndipo Inumwakhalamuli wabwino kwa iye. Ndipo lero iye akuzunzika ndikutunduzidwa,mwakuti iye sanathe kubwera ku tchalitchi.9 Ndipo, Ambuye, pamene iwo anali kupemphera mu nyumbaya Yohane Marko, kunali Mngelo anatsika kudzalowa mnyumbaya ndende, kumene Petro analimumsinga, kumeneko anatsegulazitseko,mozizwitsa, ndipo anamutsogolera iye kutuluka panja.10 OAmbuye, Inumukadali panobeMulungu. Angelo amenewoali pa kutuma Kwanu mmawa uno. Ife tikupemphera, Ambuye,kuti pamene ife tikupemphera kuno mnyumba ya Mulungu, kutiAngelo atsikire ku nyumba ya M’bale Roberson. Khumbo lakendi kukhala pamalo ake kuno, koma chosautsa chamugwirira

Page 3: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 3

iye pansi. Ndipo mulole Angelo a Mulungu amuwombole iye,amupange iye akhale bwino, kuti akhoze kudzatenganso maloake ku nyumba ya Mulungu.11 Alipo ena omwe abwera kudutsa movuta, iwo—iwo akhalaakudwala. Ndipo ife tamuwona mkazi wachikulire, pamene iyeanali pafupi kuti akhale pa mpando wake, akukweza manjaake, pamene iye amatsimphina pa mapazi ake. Iye wabwera kunyumba ya Mulungu, kuti adzachiritsidwe. Perekani, Ambuye,kuti iye apite akuyenda, wanthete ndi chitsikana cha mkaziwamng’ono.12 Ena onse amene anakweza manja awo, ambiri a iwoanakwera, chifukwa kwalembedwa, ndipo zinawerengedwapomobwereza, “Zochuluka ndi zotunduza za olungama, komaMulungu amamupulumutsa iye kwa izo zonse.” Muloleife tiulukire kutali lero mu chikhulupiriro, mikono yachikhulupiriro, imene imatiwombola ife kutichotsa ku nthendandi zotunduza zonse. Pamene msonkhano watha, pasakhalewina wofooka pakati pathu.13 Perekani, Ambuye, kuti wosakhulupirira aliyense akhalewokhulupirira. Ndipo pamene ife tikusinkhasinkha pa MawuAnu, mulole Mzimu Woyera uwatenge Iwo ndipo uwaike Iwommitima yathu, ndipo m’menemo uziwathirira Iwo kufikira Iwoasandulike chipatso cha Mawu. Tichitireni ife ichi, Ambuye,pamene ife tikuweramitsa mitu yathu modzichepetsa ndikupempha izi mu Dzina la Yesu. Ameni.

Inu mukhoza kukhala.14 Tisanalowe mu uthenga wa msonkhanowu mmawa uno, inendikufuna kuika pa malingaliro anu, moyandikira pang’ono.Ngati pali aliyense wa inu amene ali ndi matchuthi, ndipoakufuna kudzakhala nawo pa umodzi wa misokhano imeneikachitikire mu Middletown, Ohio, kuyambira Lolemba, sabata,iwo udzakakhala pa mabwalo a misasa.15 Kodi inu mukulidziwa dzina la mabwalo amisasawo, Gene?[M’bale Gene akuti, “Anati kunali thwelofu mailosi kunjakwa Middletown.”—Mkonzi.] M’bale Sullivan. Middletownndi mzinda waung’ono, ine ndikuganiza pafupifupi ngatiJeffersonville kuno. Ndi kuchimake kwa basiketibolo. M’baleSullivan ndi m’busa kumeneko. Uliwonse wa mipingo ya FullGospel, yomwe kuli sikisite chakuti ina yomwe ikuthandiziramumsonkhano uwu, adzakhoza kukuuzani inu kumene mabwaloamisasa ali.16 Ndipo kukakhala malo ogona ambiri ku mabwalo amisasako, ine ndauzidwa chomwecho, kuti akasamalire anthuomwe akufuna kubwera. Ndipo misonkhano idzayambaLolemba kudutsa mpaka Loweruka, masiku sikisi. Ndiposiidzakhalapo Lamlungu, chifukwa cha matchalitchi ena, kutiiwo akhoza kudzapita ndi kukhala ndi misonkhano yawo

Page 4: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

4 MAWU OLANKHULIDWA

ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala misonkhano yamachiritso, kapena pemphero la odwala, usiku uliwonse. Ndipoaliyense akuitanidwa. Ndipo iyo idzayamba pa Ogasiti 10,mpaka pa 15, Lolemba kudutsa mpaka Loweruka. Ndipo ngatiinu muli ndi tchuthi, ndipo—ndipo tchuthi chanu chikubwera,ndipo inu mungafune kukhala nacho mwanjira imeneyo,chabwino, ife ndithudi tidzakondwa kukhala nanu.17 Ine ndikufuna ndiwalimbikitsenso onse iwo amenesanabatizidwe mu ubatizo wa Chikhristu, kuti atsalire mmawauno ndipo aziganizire izo. Ndi kumakonzekera utumiki waubatizo umene utsatirepo mu pafupifupi maminiti forte faivitsopano, ine ndikuganiza. Izo zidzakhala pano pa tchalitchi.18 Ife kwambiri tiri poti tiziwalimbikitsa anthu kutiazibatizidwa mu ubatizo wa Chikhristu, podziwa kuti uwondi wofunikira ku chipulumutso. Pakuti kunalembedwa ndiAmbuye wathu, kutuma Kwake komaliza, kutuma Kwakekomaliza kwa Mpingo. Kapena, pamene Iye ankawutumaMpingo, kumapeto, Iye anati, “Pitani mu dziko lonse, ndipokalalikireni Uthenga kwa cholengedwa chirichonse. Iye ameneakhulupirira nabatizidwa adzapulumutsidwa.” Chotero ifetikudziwa kuti ndi zofunikira kuti ife tizibatizidwa mwakumizidwa.19 Ndipo ife tikhala osangalala kuchita ntchito iyi kwainu, kwa aliyense yemwe watsimikiza mu mtima mwawokuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu, kuti Iye anafakuti adzapulumutse ochimwa, ndipo inu ndi amene Iyeanafa kuti adzakupulumutseni; ndipo mukufuna kubwerandi kudzabatizidwa mu Dzina la Yesu Khristu kuloza kuchikhululukiro cha machimo anu; kunena, kwa dziko lapansi,kuti inu mukukhulupirira kuti machimo anu achotsedwa, ndikuti inu tsopano mukupita kukakhala wophunzira wa AmbuyeYesu, kuti mukatenge maimidwe anu.20 Ngati inu mulibe tchalitchi choti muzipitako, ife tidzakhalaokondwa kukhala nanu mu chiyanjano ndi ife. Ife tiribeumembala kuno. Ndi kachisi wotseguka, kwa Thupi lonsela Khristu, la chipembedzo chirichonse. Ife timaima ngatichipembedzo cha onse. Ndipo ife timatsegula makomokwa anthu onse, posawerengera omwe iwo ali, mtundu,fuko, kapena kachikhulupiriro, aliyense ndi wolandiridwa.“Aliyense yemwe akufuna, bwerani.” Ndipo ngati inu mulibempingo wina uliwonse, ife tidzakhala okondwa kuti inumungobwera ndi kudzayanjana nafe. Palibe chirichonse chotinkujowina. Mudzangobwera mkati muno pamene makomoatsegulidwa, ndi kudzayanjana nafe. Ndizo zonse zimene inumukusowa; mungobwera monga chomwecho. Mubwere ndimtima wotseguka, mudzaike mapewa anu pa gudumu, ndipomutithandize ife pamene tikukanikizira patsogolo pa chifukwacha Ufumu wa Mulungu. Pakuti, ife tikukhulupirira kuti

Page 5: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 5

oralo, posachedwapa liyandikira, limene zinthu zonse zimenezinayankhulidwamuBaibulo zidzakwaniritsidwa.21 Nzosakayikitsa kuti ambiri a inu munawerenga zaKhrushchev, maneno ake ku U.N., tsiku lina, mongazinabwerezedwa mowerenga kwa ine kuchokera mu pepalaya ku Canada, ndi mzanga. Iye anati, “Ngati kuli Mulungu, Iyeali wokonzeka kuti asese ndi kuyeretsapo kachisi kachiwiri,ndi inu achikapitolisiti, monga Iye anachitira pachiyambi.”Chotero tsopano inu mukhoza kuwerenga pakati pa mizere,“Iye ali wokonzeka kuti asese kachisi kachiwiri.” Ndipo nzoipa,wachikominisiti angati anene chinthu ngati chimenecho? Iyeanali ndi chinachake, ngakhalebe. Uko nkulondola. Analiachikapitolisiti, poyamba, amene anayambitsa vuto. Ife ndifeachikapitolisiti.22 Ine ndinamumva m’busa wathu wokondedwa, wapamtima,M’bale Neville, akunena ndemanga pa televizioni yake…kapena pa kulengeza kwa pa wailesi, mmawa wina,zimene zimangobwerabwera, m’malingaliro anga. Inesindikutha kuiwala basi zimenezo. Ine ndinazibwereza izokwa bwenzi la ine, usiku wapitawu. Ndipo izo zinali izi,kuti kudzakhala…Mzimu Woyera ukadzati wachotsedwa,kuchoka pa dziko lapansi, kuti chipembedzo chofunda chatchalitchi chizidzapitirirabe, osadziwa kusiyana kwake.Kodi inu munayamba, mwateropo…Ndi angati anamvazimenezo? [Osonkhana akuti, “Ameni.”—Mkonzi.] Kodi izosizinali zododometsa? Iwo sakuwudziwa Mzimu Woyera,chotero iwo sadzadziwa pamene Iwo wapita, ndipo iwoadzakhala akungopitirirabe chimodzimodzi momwemo. Pamenewotsirizayo adzasindikizidwe kulowa mu Thupi la Khristu,iwo adzakhala akupitirirabe, kuyesetsa kuti abweretseowatembenuza kwa Iwo, chifukwa iwo sakudziwa chomweIwo uli. Ndipo zipembedzo zawo zofunda zizidzapitirirabechimodzimodzi monga iwo anali. Tsopano, izo zikhozakusazimirira mwa inu monga izo zinachitira kwa ine, koma ilokwenikweni linali neno lododometsa. Kuti, iwo adzakhala kutalikwambiri zedi, basi mu miyambo ya chipembedzo, kufikirakuti iwo sadzawusowa Mzimu Woyera, chifukwa iwo sakudziwachomwe Iwo uli, kuyamba ndi kuyamba.23 Mulungu atichitire ife chifundo. M’bale, ine ndikufunakukhala mmoyo uno, ndicho chokhumba changa, kufikira kutingakhale kachidutswa kakang’ono ka kukhumudwa Kwake, inendizikadziwa iko mu mtima mwanga. Ine nditachita chinachakechimene chingamukhumudwitse Iye, ine ndizitha kuchimvereraicho mu kamphindi chabe.24 Ndiye munene, zakuti Iyeyo kulibeko; ine sindikufunakuti ndidzakhale kuno pamene Iye adzakhale kulibeko. Inendikufuna ndidzakhale nditapita pamenepo, inde, bwana,chifukwa sipadzakhala Magazi pa mpando wachifundo. Iko

Page 6: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

6 MAWU OLANKHULIDWA

kudzakhala kwa mdima ndi kwa utsi ndi kwakuda. Malo oyerasadzakhala ndi Woimirira mlandu kumeneko, kuti achondereremlandu wathu pa nthawi imeneyo. Inu mukudziwa Lembalimanena zimenezo? Malo oyera amachita utsi. Panalibe Magazipampando wachifundo, kenako ndi chiweruzo.

25 Ngati Ambuye, nthawi ina molawirira chirimwe chino,adzatipatsa ife chitsitsimutso cha mausiku angapo. Inendinangopanga izo mmalingaliro anga, ine ndikufuna kutindidzatenge Bukhu lija la Chivumbulutso, ngati phunziro paizo, kudzangodutsa Bukhu ilo la Chivumbulutso, pa.

26 Tsopano, lero, ine ndikudziwa kuti alipo ambiri abwera,kuti adzapemphereredwe. Ndipo ofesi yanga inali yotseka lero,kapena sabata ino. Ndipo anthu ena anali atabwera, sanapezemwayi woti apemphereredwe, kunja uko, chifukwa chakutianyamata anali atapita, kwa tsiku kapena chomwecho, kutiakapume. Iwo ali ndi ntchito yambiri yoti achite; ntchitoyawoyawo, kuphatikiza ntchito ya pa kachisi, ndi kuimbakwa foni yanga ndi chirichonse. Izo posakhalitsa zimakufikirammisempha mwako. Ndipo chotero ndiye ndicho chifukwachake. Ine ndikudziwa ine ndimayenera kupita kwinakwake,kamodzi mu kanthawi, ndi kukachita chinachake chosiyana,ndipo ine ndikudziwa iwo amatero, nawonso. Chotero, iwoanandiyimbira ine. Ine ndinati, “Ine ndikuganiza izo zikhalabwino.”Ndipo ife tipempherera odwala,mumphindi zingapo.

27 Ndipo ine ndinaganiza ife tiwerenge zina kuchokera kuMawu a Mulungu. Ngati inu muli ndi Baibulo lanu tsopano,tiyeni titembenuzire ku Bukhu la Yesaya. Ine ndimakondakukuwonani inu mukutenga Bukhu lanu ndi kuliwerengaIlo. Ine ndikuwerenga…Ngati inu si Mawu oposera amodzichabe kapena awiri ife tiwerenga, apobe, ndi Mawu Amuyaya,Achisavundi a Mulungu. Iwo sangathe kupita. Mutu wa 55 waYesaya, phunziro, “Chipulumutso chosatha.”

Ho, aliyense amene ali ndi ludzu, bwerani inukumadzi, ndipo iye amene alibe ndalama; bweraniinu, mudzagule, ndi kudya; eya, bwerani, mudzagulevinyo…mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo.

Bwanji inu mukutaya ndalama pa izo zimene sizirichakudya? ndipo mukugwirira ntchito chimene chirichosakhutitsa? mvetserani mwachangu kwa ine, ndipomudye inu izo zimene ziri zabwino, ndipo mulole moyowanu ukondwere wokha mu kunenepa.

Tcherani khutu lanu, ndipo mubwere kwa ine:imvani, ndipo moyo wanu udzakhala moyo; ndipo Inendidzapanga pangano losatha ndi inu, ngakhale zifundozotsimikizika za Davide.

Page 7: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 7

28 Ine ndikufuna kuti ndiyankhule ndi inu, kwa mphindipang’ono chabe, pa phunziro:Opanda Ndalama Kapena OpandaMtengo.29 Kuli zinthu zosangalatsa zochuluka kwambiri za masikuathu. Kuli zochuluka kwambiri zikukopa anthu ku zimeneife tingazitchule “zosangalatsa,” ndipo ndi za anthu onse,amisinkhu yonse.30 Kuli zokopa za achinyamata, magule amakono ndimaphwando a gwedemula, ndi nyimbo zimene iwo alinazozimene zimapita ndi izo. Ndipo zonsezo ndi zokopa, zachisangalalo.31 Ine sindikusamala kaya khomolo ndi labwino chotani limenemwanayo waleredweramo, ndi momwe iye waphunzitsidwirakuchita bwino; ngati mwana ameneyo sanalandirechomuchitikira cha Kubadwa kwatsopano, nyimbo zagwedemula zingagwire tcheru chake mwamsanga basi iyeakangozimva izo. Chifukwa, mwa iye, munabadwa mwa iye,mwa chirengedwe, mzimu wachithupithupi. Ndipo mphamvu yamdierekezi ndi yaikulu kwambiri, lero, mpaka imagwira mzimuuwo wa wamng’ono uyo.32 Ndipo ndi mochuluka motani izo zingachite kwa wamkulu,ndiye, yemwe wakana Kubadwa kwatsopano! Chifukwa,pokhapokha ngati moyo wako wasinthika, ndipo iwewatembenuka ndipo wabadwa mwatsopano, kulowa mu Ufumuwa Mulungu, chikhalidwe chako chikhalabe cha zinthu za dzikolapansi, ziribe kanthu kuti ndiwe wachipembedzo bwanji,pokhapokha ngati chimenecho chasinthidwa mwa iwe. Iweukhoza kumapembedza ndi kukhala wachipembedzo, komabeicho chidzakhala ndi mtundu wina wa mphamvu yokoka kwaiwe, chifukwa munthu wakale uyu wa tchimo ndi zokhumbazake sanafebe mwa iwe.33 Koma pamene umulola Khristu akhale pa mpandowachifumu mu mtima mwako, zinthu zimenezo sizimavutanso.Izo ndi zazikulupo kwambiri.34 Ine sindingathe kutchula dzina la munthuyo, chifukwaine sindingathe kulingalira za dzina lake tsopano, komaambiri a inu mumukumbukira iye. Iwo amati kunali chilumbakumene amuna amapitako, mwa uchifwamba, ndipo akaziamatulukirako, akuyimba. Ndipo nyimbo zawo zimakhalazodolola kwambiri, mwakuti oyenda pamadzi akamadutsa,pa ngalawa, amakhoza kupitako. Ndipo kenako asilikariachifwambawo amakhoza—amakhoza kuwagwira oyendaapamadzi awa mowadzidzimutsa, ndi kuwapha iwo. Ndipomwamuna wina wamkulu ankafuna kuti adutseko. Ndipoiye anawauza oyenda pamadzi ake kuti amumangirire iye kuchimtengo cha chinsalu cha mu sitimayo, ndi—ndi—ndi kuikachinachake mkamwa mwake, kuti iye asathe kufuula; ndi—

Page 8: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

8 MAWU OLANKHULIDWA

ndi kuika zotseka m’makutu a oyenda pamadzi ake, kuti iwoasakhoze kumva, ndi kumayenda akudutsa, kuti amve izo.Ndipo akaziwo anatulukira, akuvina ndi—ndi kumafuula,ndi kumaimba, ndipo, oh, izo zinali zopambana kwambiri,mpaka iye anazisupula khungu la mikono yake, akufuula kwaomuyendetsa ake, “Khotani! Khotani!” Koma iwo samamumvaiye, anali atatsekera mmakutu mwawo.35 Ndiyeno iye anayenda kupita ku malo ena kumene iwoanali kuti amuchotse iye, kapena, amasule manja ake, ndipoiye anali kuti achotse zotsekera mmakutu awo. Kumeneko,pamene amayenda pa msewu, iye anamva woyimba amene analiwapamwamba kwambiri kuposa ajawa uko, kuti pamene iyeamadutsanso, iwo anati, “Oh, woyendayenda wamkulu, kodi ifetikumangirireninso inu kumtengo kachiwiri?”36 Iye anati, “Ayi, ingondimasulani ine. Ine ndamvachinachake chopambana kwambiri zedi, kufikira kuti izosizidzandivutitsanso ine nkomwe.”37 Ndi mmene izo zimakhalira ndi Mkhristu wobadwa-kachiwiri. Iwo anapeza chinachake chopambana kwambirikuposa gwedemula ndi zisangalalo za mdziko lino. Iwoamasangalatsidwa ndi Mzimu Woyera. Iwo ndi wopambanakwambiri zedi, kufikira kuti dziko ndi lakufa kwa iwo.38 Koma pamene inu mupita ku zisangalalo zotchipa izi,inu mukuyenera kukumbukira kuti inu mumayenera kutengandalama zochuluka. Mnyamata wamng’ono yemwe amatengerachibwenzi chake chachikazi ku maphwando awa ndi maguleawa, ndi zina zotero, akalipira zochuluka kwambiri za malipiroake a pa sabata. Ndipo anthu achikulire amene amayeserakupeza chisangalalo popita ku mabwalo a mowa, kuti akamwekuchotsa nkhawa zawo za msabata, iwo amayenera kutiakalipire ndalama zambiri. Ndipo kodi iwo amapezako chiyanikwa izo? Iwo sapezako chirichonse komakupweteka kwamtima.39 Ndipo kumbukirani, inu mudzayenera kutimudzakambirane ndi Mulungu tsiku lina pa izo. “Ndipomalipiro a tchimo ndi imfa.” Inu simupindula chirichonse kunopa dziko lapansi, pochita zimenezo. Ndi kunyezimira kwabodza.Kumwa kumangowonjezera chisoni. Tchimo limangowonjezeraimfa pa imfa. Potsirizira panu padzakhala kulekanitsidwa ndiMulungu, Mwamuyaya, kukalowa mu Nyanja ya Moto. Ndipoinu simudzapindula chirichonse, komamudzaluza.40 NdiyeMulungu akubwera ndipo akufunsa funso, “Chifukwachiyani iwe umataya ndalama zako pa zinthu izo zimene zirizosakhutitsa? Chifukwa chiyani iwe umachita zimenezo?”41 Ndi chiyani chimawapangitsa anthu kufuna kuchitazimenezo? Iwo amawononga zonse zimene iwo ali nazo, zonsezimene iwo angakhoze kuzigwirira ntchito, kuti akagulechakumwa, kuti akamuveke mkazi wina amene iwo amayenda

Page 9: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 9

naye, kapena mtundu wina wa zosangalatsa za chidziko,chisiliro chamanyado.42 Koma ife timauzidwa mu Baibulo, ndipo timafunsidwakuti tibwere kwa Mulungu, “Ndipo kuti tidzagule chimwemweChamuyaya ndi Moyo Wamuyaya, opanda ndalama kapenaopanda mtengo.”43 Zinthu zimenezo sizingakhoze kukhutitsa, ndipo mapetoa zimenezo ndi imfa Yamuyaya. Ndipo izo zimakutheraiwe ndalama zonse zimene iwe ukhoza kuzisonkhanitsapamodzi, kuti ukhale chi—chikhwaya kapena msangalatsi,kapena mnyamata wanthabwala, kapena chirichonse chimeneiwe ukhoza kukhala, kapena mtsikana wotchuka, kapenachirichonse chimene chiri. Izo zimakutengera iwe zonse zimeneiwe ungazibweretse pamodzi, kuti uchite zimenezo. Kuvala mumavalidwe apamwamba kwambiri, ndi—ndi kuchita zinthuzimene dziko limachita, basi nkuthela kukolola cheke chachiwonongeko Chamuyaya.44 Mulungu anati, ndiye, “Chifukwa chiyani?” Kodi ifetidzachita chiyani pa Tsiku la Chiweruzo, pamene ife tititidzafunsidwe chifukwa chomwe ife tinachitira zimenezo? Kodiyankho lathu lidzakhala chiyani? Kodi lidzakhala yankholotani kwa Achimerika amakono, omwe amanena kuti iwo alifuko la Chikhristu? Ndipo pali ndalama zochuluka zimenezimawonongedwera pa mowa, mu nthawi ya chaka, kuposaza chakudya. “Chifukwa chiyani mukuwonongera ndalamazanu pa zinthu za mtundu umenewo?” Komabe, boma likhozakukutumizani inu ku ndende, chifukwa cha msonkho wamadolla asanu umene inu munatumiza mwinamwake kubungwe lina limene silinaikidwe moyenera kuti lizilandiramisonkho, potumiza wa mishonare wina kutsidya kwa nyanja.Ife tidzakafunsidwa tsiku lina, “Chifukwa chiyani iwe unachitazimenezo?”45 Ife ndife fuko la Chikhristu, ndipo mabilioni akutumizidwakwa anthu awo kumeneko, amene tikuyesera kuti tiwaguleubwanawe. Tsopano iwo akuzikana izo. NzosadabwitsaKhrushchev anati, “Ngati kuli Mulungu, Iye asesa nyumba Yakeyachifumu kenanso.” Achikunja akukhoza kupanga manenooterowo, kuti abweretse manyazi pa ife. Ndi chinthu chamanyazibwanji icho chiri! Ndipo ife tikumadzitchula tokhaAkhristu.46 Mulungu anati, “Bwerani, mudzagule Moyo Wamuyaya,opanda ndalama, opandamtengo.”Moyo, kuti mudzakhalemoyokwanthawi zonse, ndipo ife tikupotoletsa misana yathu kwa Iwondi kuseka pa nkhope Pake. Kodi ife tidzachita chiyani pa Tsikulimenelo? Kodi kudzakhala chiyani…?47 Ngati Mulungu watipatsa ife zinthu zoti tichite, ndipowatipatsa ife ndalama, ndipo watipanga ife kukhala fukololemera kwambiri pansi pa miyamba, ndiye Mulungu

Page 10: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

10 MAWU OLANKHULIDWA

adzatifunsa kodi tinachita nazo chiyani zimenezo. Chifukwachiyani ife timawonongera ndalama zathu pa zinthu zimenenzosakhutitsa? Osati kokha kwa fuko, koma izo zingakhale kwamunthu payekha payekha; kuchokera ku ndalama ya chitsulo,mpaka kumamillioni amadolla, aliyense adzapatsidwa.48 Pamene azibambo anaphana wina ndi mzake: inendinawerenga nkhani posakhalitsapa, kumene anyamata awiriamagwira ntchito mu msasa wosaka. Mmodzi anali ndi anaasanu, winayo anali ndi awiri. Ndipo mmodzi wa iwo anali wotiachotsedwe ntchito. Ndipo mmodzi wa anyamatawo yemweanali ndi ana awiri, kapena anali ndi ana asanu, anamvererakuti iye amaifunitsitsa ntchitoyo kuposa iye amene anali ndiana awiri; ndipo anapita kosaka ndi iye, ndipo anamuwomberaiye ku nsana.49 Ndalama, ndiwo mtundu wa fuko, ndiwo mtundu wakumverera, ndiwo mtundu wa mzimu umene ukuwalamuliraanthu.50 Ndiye inu mukhoza kuwona ndikofunika bwanji momweKubadwa kwatsopano kukuyenera kukhalira. “Iwe uyenerakubadwanso kachiwiri.” Izo zikuyenera kutero. “Bwerani kwaIne, ndipo mudzagule opanda ndalama.”51 Inu simungati, “Ine ndinalibe ndalama.” Inusimukusowekera ndalama iliyonse. Izo zikuperekedwamwaulere.52 Ife Achimerika tinazolowera kulipira njira yathu pachirichonse. Ndiyo mbalume yathu. “Ife timalipira pa zinthu.Ife tiri ndi ndalama.” Timawonetsera mapepala a madolla athuku maiko ena, ndi zina zotero, amene ali osauka. Ukamayenda,iwe umawona alendo akulowamo, onse atavala nthenga ndizofewa. Achimerika amapita kwa iwo. Chinthu chimenecho ndichisiliro chonyansa pamaso pa Mulungu. Zimenezo sizidzagulanjira yathu ya Kumwamba. Koma chirichonse mu Amerika, ifetimayenera kulipira njira yathu.53 Iwe ukapita ku malo odyera, ndipo iwe ukadya chakudyachamadzulo chako. Ndipo ngati iwe suyika ndalama pa tebulo,kumupatsa woperekera ameneyo, pamakhala tsinya limenelimabwera pa nkhope, pambuyo pakuti kampani yomweiye akuigwirira ntchitoyo yamulipira. Ndipo izo zimayenerakukhala pafupifupi teni peresenti, kapena kuposerapo,ya bilu yakoyo. Ngati iwe sutero, woperekera ameneyoamakuyang’anira iwe pansi ngati womana kapena winawakengati wo—wowumira. Pamene, iye amalandira ndalama zake.Ine ndikuganiza ndi chitonzo ndi chamanyazi, kuchita zimenezo.Ine ndikuganiza ndi kuweruza kolakwika kwa fukoli. Kale anali,anthu abwino, malo abwino, samalola zimenezo. Koma zonsezozikulowa mumzimu umodzi waukulu.

Page 11: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 11

54 Ine ndinali pa ulendo, pa sitima. Ndipo wolandira alendo…Ine ndinali ndi kachikwama kakang’ono mdzanja limodzi,ndi sutukesi kwinako, ndipo kabokosi ka zometera mkhwapamwanga, ndipo ndimayenda. Wolandira alendo anabwerapo,anati, “Kodi ine ndingakunyamulireni inu zimenezo?”55 Ine ndinati, “Oh, ine ndikungopita ku sitima uko, bwana.Zikomo inu, kwambiri zedi.” Basi pafupi, oh, mayadi sate.56 Iye anati, “Ine ndinyamula izo,” ndipo iye anatengachinthu chaching’onocho ndi kuchinyamulammwamba icho, ndikumayenda.57 Chabwino, pamene iye anafika, ine ndinaganizamwinamwake ine…ine ndimadziwa kuti iye amalipidwa,koma ine ndingomupatsa iye—ndimupatse iye theka la dolla. Iyemwinamwake ananyamula, katundu wangayo, kwa pafupifupi,mwina, miniti; pafupifupi kutalika kwake ngati kumapeto akachisi uno, kumene iye anakapeza sitima. Ine ndinakwera musitimayo, poyamba, ndipo ndinangofikira pansi ndi kutenga izo.Ine ndinamupatsa iye theka la dolla.

Iye anati, “Miniti chabe!”

Ine ndinati, “Ndi chiyani, bwana?”

Iye anati, “Ine ndinakunyamulirani inu zikwama zitatu!”

Ine ndinati, “Inde, bwana, uko nkulondola. Ndiye,palakwika chiyani?”58 Iye anati, “Mtengo wanga wotsikitsitsa ndi masenti twentefaifi pa chikwama. Inumuli ndi twente faifi yanga inanso.”

Mukuona, chimenecho ndicho Chimerika, chirichonsechiyenera kulipiridwa.59 Iwe ukapita koyenda mu galimoto yako ndipo iyo ikagweramu dzenje, ndipo iwe ukampeza winawake kuti akukokere iwepamtunda. Iwe uyenera kuti ukonzekere kulipira, chifukwaiwo akulipiritsa iwe chifukwa cha izo. Makako akabwera ndikudzakutenga iwe, iye akutchaja iwemwakati pa mailosi. Ndipongati ndi mlimi, kuchulukitsa kanaini pa teni, akamutulutsirathirakitale yakeyo, izo zimakhala zoipitsitsa kuposa zimenezo.60 Iwe umayenera kulipira chirichonse chimene iwewapangiridwa. Chirichonse chimakhala “Kulipira! Ndalama!Kulipira! Ndalama!”61 Ndipo komabe ndi dzenje lalitali bwanji limene tchimolakuponyanimo inu! Ndi ndani akanakhoza nkomwekukutulutsanimo inu mu dzenje la tchimo? Koma Mulunguamakutulutsanimo inu mu dzenje la tchimo, opandandalama, opanda mtengo, pamene panalibepo wina aliyenseakanakutulutsanimo inu.

Page 12: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

12 MAWU OLANKHULIDWA

62 Ngati inu simulipira mochuluka kwa galimotoyokukokaniyo, inu mukhalabe mu dzenjelo. Inu mukuyeneramukhale ndi ndalama kapena inumukhalabemu dzenjelo.63 Koma dzenje loipitsitsa limene inu munayambamwagweramo, ndi limene mdierekezi anakuponyeranimo inu,dzenje la tchimo ndi kusakhulupirira. Mulungu mwachifuniroadzakutulutsanimo inu, opanda ndalama, opanda mtengo.Ndipo komabe inu mwangogona mu dzenje, mukungosambiramu tchimo, ndipo simukuitanira nkomwe pa Iye.64 Pamene inu mupeza galimoto yokukokaniyo, kawirikawiriiwo amaika tcheni chachikulu kulowa mdzenjelo,amachikulunga icho mozungulira bampala kapena zina zotero,ndi kuyamba kugwejemula. Ndipo mphamvu ya galimotoyoimayamba kukoka, ndipo injini zimayamba kugwira ntchito,ndi kukukokerani inu panja.65 Pamene Mulungu akupezani inu mu dzenje la tchimo, ndiponakumvani inu mukuitanira pa Iye, Iye amatumiza tchenichimene chinakulungidwa mozungulira Kalvare, chikondi chaMulungu, ndipo amadzachikoletsa Icho pa mtima wanu,ndipo amadzaika Mphamvu ya Mzimu Woyera kumeneko,kuti iyambe kukoka. Ndipo izo simulipira kalikonse. Ndipokomabe ife timagona mu dzenje chifukwa ife sitingathe kulipiraizo ndi matumba athu. Ife Achimerika timaganiza kuti ifetikhoza kulipira izo kuchokera m’matumba mwathu, koma inusimungathe. Ndi zopanda ndalama kapena zopanda mtengo. Inusimulipira izo ku tchalitchi. Yesu analipira izo pa Kalvare. Komaanthu akuchitamanyazi ndi Izo. Iwo akufuna Izomwanjira yawoyawo. Mulungu ali nayo njira yoti inu mulandirire Izo, ndipo Izondi zaulere ngati inu mungazitenge Izo.66 Kawirikawiri, pamene iwo akukoka iwe mu dzenje,iwe umakhala utakandikandika, iwe umayenera kupita, kuchipatala. Ndipo iwo asanayambe kugwira ntchito pa iwe,chinthu chimodzi chisanachitike, iwo amafunsa, “Kodi atiapereke bilu ndi ndani? Ngati ife titi tisoke mabalawa, ngatiife titi timuthire mafutawa, ndi kumubaya kuti—kuti tikubayeiwe katemera wa chiphe cha magazi, kodi iwe uli ndi inshuransiya mtundu wanji?” Iwo asanachite chinthu chimodzi, payenerapakhale ndalama pa mzere.67 Koma pamene Ambuye wathu aika tcheni chake chachikondi mozungulira mtima wako, ndi kukukoka iwekuchokera mu dzenje la tchimo, Iye amachiritsa mtimawosweka uliwonse, amachotsamo tchimo lonse. Ndipo biluyoimakaikidwa mu nyanja ya kuiwala, kuti asadzakumbukirensonkomwe za iwe. “Bwerani, opanda ndalama kapena opandamtengo.” Ziribe kanthu kuti iwe wachekedwa moyipa chotani,ndipo wavulazidwa moyipa bwanji, mmene banja lako lachitira,kapena zimene iwe wachita, palibe bilu kwa izo. Iye amachiritsa

Page 13: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 13

kupweteka kwa mtima konse, amachotsa zisoni zako zonse. “Iyeanavulazidwa chifukwa cha mphulupulu zathu, anatunduzidwachifukwa cha kusaeruzika kwathu; chilango cha mtenderewathu chinali pa Iye; ndipo ndi mikwingwirima Yake ifetinachiritsidwa.” Zonsezo ndi zaulere.68 Ndipo ife sitilandira Izo, ndi chifukwa chakuti ifetikulamulidwa ndi mzimu woipa. Ife tikulamulidwa ndi mzimuwa fuko, mzimu wa dziko lapansi, mmalo moti tizilamulidwandi Mzimu wa Mulungu, Mzimu Woyera, umene umatitsogoleraife ndi kutilondolera ife ku Zoonadi zonse, ndi kulipangitsaBaibulo kutero.69 Nthawiina m’mbuyomo, ine ndinali kuyankhula ndiwachikunja. Iye anati, “Taganizani za ichi, Bambo Branham.Zosautsa zonse izi za moyo, ndipo chinthu chokhacho chimeneife tiri nacho, chimene ife tinapulumuka nacho, ndi zolembedwazina za Chiyuda zachikale.”70 “Oh,” ine ndinati, “bwana, zimenezo zikhoza kukhalazonse zimene inu muli nazo, koma ine ndiri nacho chinachoposa zimenezo. Ine ndiri ndi Mzimu wa Iye amene analembaIzo, zimene zimatsimikizira Izo ndi kuzipanga Izo kukhalachomwecho, lonjezo lirilonse.” Iye sanadziwe mmene iye akanatiazitengere izo.71 Mukuona, inu mukuyenera mubwere ndipo mudzaguleopanda ndalama, mudzagule opanda mtengo. Izosizikutengerani inu kalikonse. Izo ndi zaulere kwa “aliyenseyemwe akufuna, muloleni iye abwere.” Mulungu akukukokaniinu kuchokera mu dzenje.72 Monga munthu uja pa chipata chotchedwa Chokongola.Iye anali ataponyedwamo, kuchokera m’mimba ya amayi ake,ndi mdierekezi yemwe anamulumalitsa iye kumapazi ake.Njira yake yopezera zinthu inali kupempha zithandizo kwaanthu omwe amadutsa. Ndipo pamene iye anakhala pa chipatammawa umenewo, iye anawona alaliki awiri achipentekositeakubwera. Analibe khobiri limodzi pakati pawo, pakuti iyeanati, “Siliva ine ndiribe.” Ndipo khobiri ndi kachidutswakakang’ono kwambiri ka siliva. “Siliva ndi golide ine ndiribe.”73 Ine ndikuganiza munthuyo anaganiza chinachake chongaichi. “Palibe chifukwa chonyamulira chikho changa.”Mwinamwake iye anali kuyesetsa kuti asunge ndalamazokwanira. Iye anali usinkhu wa zaka forte zakubadwa, ndipomwinamwake iye amayesetsa kuti asunge ndalama zokwanira,a dokotala akanakhoza kumupangira iye zochirikiza ziwiri, kutiiye aziyenderapo, pakuti, iye, mu mfundo za kumapazi kwakendi mmene iye anafowoketsedwamo. Ndipo mwinamwake iyeankayenera kuti akhale ndi ndalama, kuti akhale pa mzere,madokotala asanamupatse iye chithandizo. Ndipo ndithudipanalibe chifukwa choti iye azigwirabe chikho chake kwa alaliki

Page 14: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

14 MAWU OLANKHULIDWA

achipentekosite awa omwe analibe kalikonse. Mwayi, iwo a…anali osauka kwambiri, sakanapeza nkomwe khobiri kuchokerakwa anyamata amenewo.74 Koma pamene iye anayang’ana mu nkhope zawo! Mmodzi,wamng’ono ndi wamanyazi ndi ubwana; mmodzi winayo,wokalamba ndi wamakwinya; pamene Yohane…pamene Petrondi Yohane amapita ku chipata. Iye anawona chinachake mwamwamuna wachichepereyo. Ndicho, kuchita manyaziko kunalikopambana pang’ono kuposa kwa wamba. Iye anawona pansipa makwinyawo ndi nkhawa, za dzuwa la Chigalileya limenelinali litawotcha nkhope ya nsodzi wokalambayo, pamenepopanali “chimwemwe chosaneneka, ndi ulemelero wozadza.” Iyeanawona chinachake chimene chinawoneka chosiyaniranapopang’ono.75 Inu mukudziwa, pali chinachake ndi Chikhristu, chimenechimawapangitsa anthu kuwoneka mosiyana. Iwo ndi anthuokongoletsetsa mu dziko lonse.

Ndipo iye anatenga chikho chake ndipo anangochigwiritsitsaicho.76 Ndipo mtumwi Petro, pokhala wamkulu kwambiri, anati,“Siliva ndi golide ine ndiribe.” Mwakulankhula kwina, “Inesindingakuthandize iwe chirichonse, kuti ukagulire ndodozoyendera izi. Siliva ndi golide ine ndiribe, koma chimeneine ndiri nacho!” Iye anali atapita kukagula kwa Iye ameneanali ndi uchi ndi zimwemwe za vinyo wa chipulumutso.Iye anali atangobwera, masiku awiri kapena atatu izozisanachitike, kuchokera ku Pentekosite, kumene chinachakechinali chitachitika.77 Ndipo mnyamatayo analumpha ndi “ameni” wamkulukwambiri ndi izo, ndipo anayang’ana pa nkhope yake.78 Chinachitika ndi chiyani? Unyolo uja wa chisoni, chifundocha Iye amene anati, “Ine ndinali ndi chifundo pa odwala,”Mzimu womwe uja unali utatenga malo mu mtima mwa nsodziwakaleyo. Iye anati, “Ngati ziri za ndalama, ine ndiribe iliyonse,koma ine ndiri ndi chinachake chimene chiti chitenge malo akekamillioni. Chomwe ine ndiri nacho!”79 Tsopano kumbukirani, Petro anali Myuda, ndipo iwoamakonda ndalama, mwachirengedwe, koma Myuda uyuanali atatembenuka. Osati, “Chomwe ine ndiri nacho, inendikugulitsa iwe.”80 Koma, “Chomwe ine ndiri nacho, ine ndikukupatsa iwe!Chomwe ine ndiri nacho! Ine ndiribe khobiri mthumbamwanga.Ine sindingathe kugula lofu ya buledi. Ine sindingathe kugulachirichonse. Ine ndiribe senti. Koma ngati iwe ungalandireizi, chomwe ine ndiri nacho, ine ndipereka kwa iwe chifukwaicho chinapatsidwa kwa ine.” Ndicho chimene ife tikusowa.“Chomwe ine ndiri nacho, ine ndikupatsa iwe.”

Page 15: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 15

“Kodi muli ndi chiyani, bwana?”81 “Ine ndinali uko kwa Iye amene amagulitsa mkaka ndi uchi,opanda mtengo. Ine ndipereka Izo kwa iwe. Iwe ulibe chotiundipatse ine pa Izo. Ngati iwe ungalandire Izo, ine ndikupatsaiwe Izo. Osati ngati wina amene angaikepo mtengo, koma iwoamene angapereke.”82 Chifukwa, “Monga mwaulere mmene inu mwalandirira,mwaulere perekani.” Iko kunali kutuma kwa Ambuyewake, basi masiku atatu chabe apitawo. “Pitani mu dzikolonse, mukalalikire Uthenga. Iye amene akhulupirira ndiponabatizidwa adzapulumutsidwa; ndipo iye amene sakhulupiriraadzawonongedwa. Zizindikiro izi zidzawatsatira iwo ameneakhulupirira: Mu Dzina Langa iwo adzatulutsa ziwanda; iwoadzayankhula ndi malirime atsopano; ngati iwo adzamwazinthu zakupha, izo sizidzawapweteka iwo; ngati iwo adzatenganjoka, iyo siidzawavulaza iwo. Monga mwaulere mwalandirira,mwaulere perekani.” Myuda ameneyo anali atasinthidwa.[M’bale Branham akugogoda paguwa kanai—Mkonzi.]83 Chimene ife tikusowa mu Amerika ndi kusinthika, kwaMzimu Woyera kuti utenge malo a timiyambo tathu tina tachipembedzo. “Monga mwaulere inu munalandirira, mwaulereperekani.”84 “Chomwe ine ndiri nacho, ine ndikukupatsa iwe: MuDzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, dzuka ndipo uyende”;chikhulupiriro mu Dzina losaipitsidwa la Mlengi lija!Nzosadabwitsa iye anapita akutsimphina ndi kulumpha, ndipoakutamanda Mulungu!85 Oh, inu mukudziwa zinthu zazikulu, iye mwinamwakeanali atakhala pamenepo zaka forte, akuyesera kuti apezendalama zokwanira kuti adzigulire ndodo zinazake, komaiye samatha kuchita zimenezo. Koma pomwepo pa maloosayembekezeka kwambiri, ndi nthawi yosayembekezeka, ndianthu osayembekezeka, osakwanira, iye anapeza chimene iyeankachifuna. Ndine wokondwa kuti Mulungu amachita izomwanjira imeneyo.86 Ndipo kagulu ka apang’ono, otchedwa-odzigudubuza usikuwina, ine ndinapeza chimene ine ndinkachifuna, ndalamaimeneyo siikanakhoza kugula. Mu gulu la osazindikira,osaphunzira, anthu ovala mwaumphawi, Akuda, kuyambandi kuyamba, kunja uko mmalo ochezeramo otembenuzidwaaang’ono, pansi, ine ndinadzapeza mtengo, ngale; pamenewakuda wokalamba uja anadzayang’ana mmaso mwanga, ndipoanati, “Kodi iwe unalandira Mzimu Woyera chikhulupirireni?”Oh, Ichi chinali chinachake chimene ine ndinkachifuna. Inesindinkayembekeza kuti ndikanachipeza Icho pakati pa anthuamenewo, koma iwo anali nacho chimene ine ndinkachisowa.

Page 16: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

16 MAWU OLANKHULIDWA

87 A U.N. lero, iwo sangavomereze chimene ife tiri nacho,koma ndi chomwe iwo akuchisowa. Khrushchev, ena onse aiwo, akusowa Khristu, mu ubatizo wa Mzimu Woyera. Iwousintha zikhalidwe zawo. Iwo uwapanga amuna, omwe iwoamawada, kukhala abale. Iwo uchotsapo dyera, ndi nkhwidzindi mikangano; ndipo uyikamo chikondi ndi chimwemwe, ndimtendere, ubwino ndi chifundo.88 Inde, mmalo osayembekezeka, nthawizina iwe umapezamochimene iwe umachifuna.89 Kodi ana a Israeli akanapereka chiyani (zofunkha zonseza ku Igupto) pamene milomo yawo inkaukha magazi,pamene lirime lawo limalendewera mkamwa mwawo? Iwoakanatha kupereka golide yense amene iwo anawalandaAigupto, chifukwa cha kumwa kumodzi kwa madzi abwinoozizira. Atsogoleri awo a mchipululu anali atawatsogolera iwokuchokera ku thamanda kupita ku thamanda, kuchokera kumaenje kupita ku akasupe, komamonsemomunalimutawuma.90 Kenako apo panabwera, opanda ndalama kapena opandamtengo! Liwu linayankhula kwa mneneri ndipo linati,“Yankhula kwa thanthwe,” chinthu choumitsitsa mu chipululu,chinthu chakutali kwambiri ndi madzi. Pamenepo ludzulawo linathetsedwa, opanda ndalama kapena opanda mtengo.“Yankhula kwa thanthwe.” Osati ulipire kwa thanthwelo, koma“uyankhule kwa thanthwelo.”91 Iye akanalibe Thanthwe usikuuno. Iye ndi Thanthwe mudziko lotopetsa. Ngati inu mukuyenda mu dziko lotopetsalimenelo, yankhulani kwa Thanthwe. Simukusowa kumulipiraIye; yankhulani kwa Iye. Ndipo Iye ndi thandizo lopezekeratumu nthawi ya mavuto. Ngati inu mukudwala, yankhulani kwaThanthwe. Ngati inu mukudwala ndi-tchimo, yankhulani kwaThanthwe. Ngati inumwalema, yankhulani kwaThanthwe.92 Mukuona, zimaoneka ngati izo zikhala paliponse…Izozimawoneka ngati, ngati kunalibe madzi kumusi ku maloochepa amene kunali akasupe, sikukanakhalamadzi pamwambapa phiri ilo, mmphepete mwa thanthwe. Mulungu amachitazinthu mobwerera mmbuyo basi kwa zomwemunthu akuganiza.Thanthwe, malo owumitsitsa mu chipululu, koma Iye anati,“Yankhula kwa Thanthwe.”93 Lero, anthu anyengedwa kwambiri. Iwo amaganiza ngatiiwo angapite ndi kukanena mapemphero awo, kukamulipirawansembe wina kuti anene mapemphero angapo a iwo,kulipira njira yawo kuti adutse. Ngati iwo angamangetchalitchi china chachikulu kwinakwake, ndipo munthu winawolemera nathandizira icho, kumapitirira kumakhala muchisiliro, kukhala ndi winawakenso woti azimupemphereraiye, iye amaganiza kuti ndi zimenezo. Mulungu samafunandalama zanu zonyansa. [M’bale Branham akugogoda pa guwa

Page 17: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 17

katatu—Mkonzi.] Chinthu chonse chimene Iye akuchifuna ndikudzipereka kwanu ndi moyo wanu kuti uziyankhula kwaIye. Mulungu wakupatsani inu ndalama, inu musawonongereizo pa zinthu zimene sizikhutitsa. Muziwonongere izo pazinthu zimene zimakhutitsa. Koma kubweretsa kukhutitsidwakwenikweni, inu simungakupeze iko kufikira inu mutayankhulakwa Thanthwe.94 Iye anabweretsa madzi-opereka moyo, opanda ndalamakapena opandamtengo.Ndipo iwo anamwa, ndipo ngamila zawozinamwa, ndipo ana awo anamwa, ndipo anakhalabe kasupeakuyenderera mu chipululu.95 Ndipo chomwechonso Iye ndi Thanthwelo lero, mu dzikolotopetsa ili, kwa anthu amene akuwonongeka. “Aliyense ameneakhulupirira pa Iye sadzawonongeka, koma adzakhala nawoMoyo Wamuyaya.”96 Zindikirani. Usiku uliwonse, iwo sankasowa kutiazisinkhasinkha za mkate. Mkate wawo umabweretsedwa kwaiwo, usiku uliwonse, watsopano.97 Ife timapita lero kukagula lofu ya buledi. Ngati iwe uliwopemphetsa, ndipo iwe ukapita ku sitolo uko, ndi kukati, “Inendikufuna lofu ya buledi.”98 Iye akhoza kunena kuti, “Ndiwonetse ine, kaye poyamba,ndalama yako. Ine ndikuyenera ndikhale ndi ma senti twente-faifi pa lofu ya buledi iyi.”99 Ndipo inu mumapeza chiyani mukagula iyo? Ichi ndichakumbali pang’ono, koma inu mumapeza chotsikitsitsachimene tirigu angapange. Iwo amachotsamo ma—mavitaminionse mwa iye, deya yense, ndi kumupereka iye kwa nkhumba.Amasakaniza ka mulu ka zomata komwe kamamata deyayopamodzi, ndipo amamusefa iye, ndi kupanga lofu ya buledi,wopangidwa ndi manja auve, awutchisi, nthawi zambiri. Inumukuona zimene inu mumazipeza mu buledi wanu, nthawizina,mibulu ya tsitsi, ndi zinthu zachiwerewere, ndi tizidutswatokulungira, ndi china chirichonsecho chimene chimagweramophikira mmenemo. Anthu ochimwa okhala ndi matendaopatsirana pogonana, ndi chirichonse, kuzisakaniza mmenemo.Ngati inu mutawona iye akupangidwa, inu simungathe nkomwekumudya iye. Ndipo, komabe, inu mumalipira masenti twente-faifi anu kapena inu simumupeza iye.100 NdipoMulungu amawadyetsa iwo usiku uliwonse, ndimkatewopangidwa ndi manja a Angelo; opanda ndalama, opandamtengo. Ndipo, lero, mkate umenewo ukuimira Khristu, Moyowauzimu, anatsika kuchokera Kumwamba, kuti adzaperekeMoyo Wake.101 Ndipo Mulungu amawapatsa ana Ake, tsiku ndi tsiku,chowachitikira chatsopano. Inu mukukumbukira, ngati iwoawusunga mkatewo, iwo umawonongeka.

Page 18: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

18 MAWU OLANKHULIDWA

102 Inu mumamva wina akuyankhula zakuti, “Chabwino, inendiri…Ine ndikuuzani inu. Ndine wa Chilutera. Ndine waChipresibateria, Baptisti. Ndine wa Chipentekosite,” imeneyondi lofu ya buledi chabe yopangidwa ndi dzanja la munthu.Ndizo zonse zomwe ziriko kwa izo, zonyansa basi, ndizopangidwa ndi manja a anthu.103 Koma pamene iwe umva chokuchitikira cha umboni,watsopano, “Mmawa uno, mu pemphero, Mzimu Woyeraunabatiza moyo wanga mwatsopano,” oh, m’bale, chimenechondi Chakudya cha Angelo. Iye amawadyetsa iwo mwatsopano,tsiku ndi tsiku, kuchokera Kumwamba.

Mivumbi ya madalitso ife tikuifuna.Madontho a chifundo motizungulira ifeakugwa,

Koma pa mivumbi ife tikuchonderera.104 Oh, inde, tumizani kuchokera Kumwamba, yatsopano,Ambuye, Khristu Mkate wa Moyo. Muwuponyere Iwo mu mtimamwanga, ndipo mundilole ine ndikondwerere Kukhalapo Kwakekwakukulu.105 Ndithudi, iwo anali othokoza. Iwo anali oyamikira. Ndipomwamuna aliyense kapena mkazi amene wabadwa mwa Mzimuwa Mulungu, ndi kulandira Mzimu Woyera, nthawizonseadzakhala wothokoza. Ziribe kanthu kuchitika chiyani, inumudzakhala oyamikira.106 Monga mnyamata wamng’ono, wakhungu uko ku mapiri,Benny wamng’ono, iye anabadwa. Pafupifupi usinkhu wamiyezi eyiti yakubadwa, ng’ala inayamba kumayala mmasomwake. Makolo ake anali osauka. Iwo amakhala mmbalimwa phiri la makande. Ndipo iwo ankadziwa kuti maopareshoni amenewo akanakhoza kupulumutsa maso a Bennywamng’onoyo, kuti azikhoza kupenya. Iye anali mnyamatatsopano wa pafupifupi usinkhu wa zaka thwelofu zakubadwa.Makolo ake amangokwanitsa zokwanira zopezera buledi ndinyama pa chaka. Iwo sakanakwanitsa opareshoniyo.107 Oyandikana nawo onse, pamodzi, amamuwona Bennywamng’ono akumayesera kusewera ndi tiana tating’ono kunjauko, wakhungu. Iye samatha kuwona zimene iye amachita.Iwo amamva naye chisoni. Ndipo mmodzi aliyense, chakachimenecho, anaikamo kagawo kakang’ono kowonjezera kambewu. Iwo anagwira ntchito molimbikirapo pang’ono mudzuwa. Ndipo pamene mbewu zinagulitsidwa mu chilimwe, iwoanatenga ndalamazo ndipo anamuika Benny wamng’ono pasitima, ndi kumutumiza iye kwa adokotala.108 Iwo anachita opareshoniyo ndipo inayenda bwino.Ndipo pamene iye ankabwererako, oyandikana nawo onseanasonkhana pamenepo pamene Benny wamng’ono amatsika

Page 19: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 19

sitima. Maso ake aang’ono owala, akunyezimira. Iye anayambakufuula ndi kulira, pamene iye amayang’ana pa nkhope zawo.109 Mmodzi wa makondakitarawo anati, “Mwana,zinakutengera ndalama zingati opareshoni imeneyo?”110 Iye anati, “Bambo, ine sindikudziwa zomwe zawatengeraanthu awa. Koma ndine wokondwa kuti ine ndikutha kuwonankhope zawo, omwe analipira mtengo wake.”111 Umo ndi mmene ife timamverera. Ine sindikudziwa chomweIzo chinamutengera Mulungu. Ine ndikudziwa Iye anandipatsaine chopambana chomwe Iye anali nacho, Mwana Wake.Koma ndine wothokoza kwambiri kukhala ndi kupenyakwauzimu uku, kuti ine ndikutha kupenya mu nkhope Yakendi kudziwa kuti Iye anandifera ine. Ine sindikudziwa zomweIzo zinamutengera Iye. Ife tiribe njira yoti nkuziwerengeraizo. Mtengowo unali waukulu kwambiri. Ine sindingathekukuuzani inu momwe iwo unaliri. Koma ndine wothokoza.Ndine woyamikira, kuti, m’menemo ine ndinali wakhungunthawiina, ine tsopano ndikutha kupenya.112 Ndine woyamikira kuti pamene a Mayo Brothers anandiuzaine kuti nthawi yanga yatha, pamene madokotala anandiuzaine kuti ine sindingathenso kukhala moyo, zaka twente-faifi zapitazo, ine ndiri moyo lero. Ine sindikudziwa zomwezinamutengera Mulungu, koma ndine wothokoza kuti inendiri moyo.113 Nthawiina ine ndinali wochimwa, womangidwa mutchimo, ndi kupweteka kwa mtima, kumawopa imfa. Koma,lero, imfa ndi chigonjetso changa. Aleluya! Iyo ikhozakokha kundibweretsa ine mu Kukhalapo kwa Iye yemweine ndimamukonda, kuti ine nditha kuyang’ana pa nkhopeYake. Iye anasintha chinthucho, ndi opareshoni, Iye anatengamtima wanga ndipo anawupanga iwo kukhala watsopano. Inendikudziwa chinachake chinachitika kwa ine.114 Mu pepala kugwa kwa masamba kwapitaku, mu Minnesota,kumeneko kunali mnyamata wamng’ono yemwe anatenganjinga yake ndi kupita ku tchalitchi mmawa wina, ku Sandesukulu. Mwamuna wamng’ono wina mwa oyandikana nawo,iye analibe chochita ndi Sande sukulu, iye anamutenga bwenziwake wamkazi ndipo anapita kumakasewera pa ayezi. Ndipobamboyo anali munthu wachikulire, ndipo iye anafika pa ayeziwopyapyalayo ndipo anagwapo. Iye anali atamuseka mnyamatawamng’onoyo mmawa uja pamene iye amayenda mu msewu,anamuuza bwenzi wake wa mkazi, anati, “Ndi kagulu kaotentheka ako kakupita ku tchalitchi icho.” Ndipo pamene iyeanagwa pa ayezi, bwenzi lake la mkazi anali kutali ndi iye. Iyeanali wopepuka; iye anadutsapo. Koma pamene iye anabwerandi kudzaika mikono yake pa ayezi, iye anawumapo, ndipoanatsakamira pa ayeziyo.

Page 20: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

20 MAWU OLANKHULIDWA

115 Bwenzi wake wa mkazi anayesera kuti amugwire iye, komaiye anali wolemera kwambiri, mkaziyo amaswa ayeziyo. Iyeanamufuulira iye, “Bwerera! Bwerera! Iwe ugwera mkati, ndipoife awiri tonse timira.” Iye anafuula, iye analira, ndipo panalibechoti nkumuthandiza iye.116 Patapita kanthawi, uko pamwamba pa phiri, panabwerakanjinga kakang’ono, kakupalasa, mnyamata wamng’ono alindi Baibulo mkhwapa mwake. Iye anamva mifuuyo, ndipoiye anathamangitsa njinga yake yaing’ono. Analiyika Baibulolake pansi, ndipo anathamangirako pa ayezi. Anakwawapamimba yake yaying’ono, atavala zovala zake zabwino, mpakaanagwira mikono ya bamboyo, ndipo anapitirira kumukokeraiye m’mbuyo, kufikira iye anamutulutsamo iye mu ayezimo.Anathamangira uko ndi kukaimitsa galimoto. Iwo anaitanitsaambulasi ndipo anamutengera iye ku chipatala.117 Iye atatha kupita ndi kukalipira ambulasi, anawalipiramadokotala chifukwa cha majekeseni a chibayo ndi zinthuzimene iye ayenera kuti anampatsa, iye anabwera kwamnyamata wamng’onoyo. Iye anati, “Mwana wanga, kodi inendiri ndi zako zingati?”

Iye anati, “Palibe.”118 Iye anati, “Ine ndiri nawe ngongole ya moyo wanga.”Taganizani za zimenezo. Ndalama sizikanatha kulipira izo.Unali moyo wake.119 Umo ndi mmene ife tikuyenera kumamvererera kwaMulungu. Osati kuti tigule njira yathu ndi chinachake; komaife tiri naye ngongole Mulungu ya moyo wathu, pakuti ife tinalikufa ndipo tinkamira mu dzenje la tchimo. Mulungu anaponyeramikono Yake ndi mwinjiro pa ine.

Ine ndinali kumira mozama mu tchimo,Kutali ndi gombe la mtendere,Nditadetsedwa mwakuya kwambiri mkatimu,Kumira koti sindidzadzukanso;Koma Mbuye wa mnyanjaAnamva kulira kwanga kosimidwa,Kuchokera mmadzi ananditukula ine,Tsopano ndine wotetezeka.

120 Ine ndiri naye Iye ngongole ya moyo wanga. Inu muli nayeIye ngongole ya moyo wanu. Inu muli naye Iye ngongole yamoyo wanu, kuti muzimutumikira Iye; osati kuupereka iwo,kumayendayenda ndi kumadzibwekerera za chipembedzo chanucha tchalitchi; osati kumayendayenda ndi kumawatsutsa ena;koma kuyesera kuti muzitumikira ndi kuwapulumutsa ena, ndikuwabweretsa iwo ku chidziwitso chaAmbuyeYesuKhristu.121 Mwana wolowelera. Potseka, ine ndikhoza kunena ichi.Pamene iye anali atawononga chuma chake chonse, chuma chaabambo ake, ndi kukhala kwa chisokonezo, ndipo pamene iye

Page 21: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 21

amabwerera kwawo…Iye amagona mu khola la nkhumba,ndipo iye anabwera pozizindikira yekha. Ndipo iye anati,“Ndi antchito angati olembedwa, abambo anga alinawo,amene alinazo zochuluka zosunga, ndipo ndine pano ndikufa,chifukwa chosowa.” Bwanji ngati iye akanayesera kunena kuti,“Ndikudabwa ngati ine ndiri ndi ndalama zina zomwe inendingathe kukawabwezera abambo (zomwe ine ndinawonongapothawa) ndi izo?” Koma iye amadziwa chikhalidwe chaabambo ake, ndipo iye anati, “ine ndidzuka ndipo ndipita kwaabambo anga.”122 Abambowo sanati, “Dikira miniti, mwana! Kodi iweukudzabweza ndalama zanga?” Ayi. Iye sanamuwerengere iyemachimo ake. Iye anali wokondwa kuti iye amabwerera. Iyeanali wokondwa kuti iye wafika podzizindikira yekha, chifukwaiye anali mwana wake. Iye anali mwana wake yemwe. Iye analiwokondwa kuti iye anali pa njira yake ya kwawo. Tsopano, iyesanavomereze tchimo lake, koma iye anali wokondwa pameneiye anabwera podzizindikira yekha ndipo anati, “ine ndachimwapamaso pa Mulungu wanga, ndi pamaso pa abambo anga. Inendidzuka ndipo ndipita kwa iwo.”123 Ndipo pamene iwo anamuwona iye, patali, iwoanathamangira kwa iye ndipo anamupsyopsyona iye.Ndipo iwo anati, “Muphe mwana wang’ombe wonenepayo,”opanda ndalama. “Mundibweretsere mwinjiro wapamwambakwambiri,” opanda ndalama. “Mundibweretsere mphete,”opanda ndalama, “muiveke iyo pa chala chake. Tiyeni ife tidye,timwe, ndipo tikondwere, pakuti mwana wanga uyu anatayikandipo tsopano wapezeka. Iye anali wakufa, ndipo tsopano iye alindi moyo kachiwiri. Tiyeni ife tikondwerere izo.”124 Ndinene ichi abwenzi, kuti nditseke. Chinthu chokhachochimene chimakhutitsa, zinthu zenizeni zokhazo zomwe ziripo,zinthu zabwino zokhazo zomwe ziripo, sizingathe kugulidwandi ndalama. Izo ndi mphatso zaulere za Mulungu, mwa YesuKhristu: chipulumutso cha moyo; chimwemwe. Bwerani ndipomudzadye, ndipo mudzakhutitsidwa.

Chifukwa chiyani inu mukuwonongera ndalama paizo zimene siziri chakudya? ndikugwirira ntchito yanupa izo zimene sizimakhutitsa? mverani mochirimikakwa ine, ndipo mudzadye…izo zimene ziri zabwino,ndipo mulole mtima wanu ukondwere wokha mukunenepa uko.Tcherani makutu anu, ndipo mubwere kwa ine:

imvani, ndipo solo yanu idzakhala moyo; ndipo inendidzapanga pangano losatha ndi inu, ngakhale zifundozokhazikika za Davide.

125 Zinthu zonse zomwe ziri zokhalitsa, zinthu zonse zomweziri zabwino, zinthu zonse zomwe ziri zokondweretsa, zinthu

Page 22: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

22 MAWU OLANKHULIDWA

zonse zomwe ziri Zamuyaya, ndi zaulere, ndipo simulipirachirichonse. Kumapeto a kulemba kwa Bukhu ili, Ilo linati,“Aliyense amene akufuna, muloleni iye abwere ndipo adzamwekuchokera ku Madzi a kasupe a Moyo, kwaulere,” opandandalama, opanda mtengo. Chifukwa chiyani inu mumawonongandalama pa izo zomwe sizikhutitsa, ndi kulola zinthu zenizenizimene zimakhutitsa, zaulere, zipite zosasamalidwa ndi inueni?

Tiyeni ife tipemphere.126 Pamene inu muli chete ndi mu pemphero, kodi alipo, muchipinda chino, mmawa uno, iwo amene sakumwa kuchokeraku Kasupe ameneyo, amene zokhumba za dziko zikanalibem’moyo mwanu, ndipo inu mukufuna musinthe malo anuomwerapo, mmawa uno, kapena katapira wa ndalama zanu?Inu mukufuna kuti mubwere ndi kudzagula kuchokera kwaMulungu, (opanda ndalama, opanda mtengo), uchi ndi mkaka,zimwemwe za vinyo?Kodimungakwezem’mwamba dzanja lanu,ndikuti, “Mundikumbukire ine, M’bale Branham, pamene inumukupemphera”? Mulungu akudalitseni inu, bwana. Mulunguakudalitseni inu, bwana. Mulungu akudalitseni inu, mlongo.Alipo ena omwe angati, “Ndikumbukireni ine, M’bale Branham,pamene inu mukupemphera”?127 Ena a inu anyamata, eya, amene mwaononga moyo wanu.Ma—ma—ma ora amene amayi anakhala mu pemphero chifukwacha inu, ndi abambo, kuphunzitsa konse kumene kunachitikapa inu, ndipo komabe inu mwazitaira izo kumbali, kutimuzimvetsera ku kunong’oneza kwa mdierekezi. Tsopano inumukukhumba nyimbo za mdziko, zinthu za mdziko. Ndipo inumukubwera podzizindikira nokha, monga wolowererayo mukhola la nkhumba. Kodi inu mungakweze dzanja lanu, mlongo,m’bale, ndikuti, “Mulungu, ndikumbukireni ine. Ndibweretseniine kwa inemwini, mmawa uno, mundilore ine ndibwere kunyumba ya Atate anga”? Izo sizikutengerani inu chinthuchimodzi. Iye akuyembekezera inu. Ziribe kanthu zimene inumwachita, “Ngakhale machimo anu akhale ngati kapezi, iwoadzayera ngati matalala; ofiira ngati magazi, iwo adzayera ngatiubweya wankhosa.” Kodi iwo ali mu Kupezeka kwa Umulungu,amene angakweze dzanja lawo?128 Iwo amene akudwala ndi osowa, anene, “ine—inendinagwera mu dzenje. Satana wa—wachita choyipa kwaine. Iye wandilumalitsa ine ndipo wandidwalitsa ine, kapenachinachake. Ine ndikukhumba, mmawa uno, unyolo wachikhulupiriro cha Mulungu kuti usunthire mu mtima mwanga,kuti undikokere m’mwamba ine kundichotsa mu dzenje ili,monga mwamuna wa pa chipata chotchedwa Chokongola.”Kwezanimanja anu.Mulungu akudalitseni inu, aliyense.129 Ambuye, ine ndikubweretsa kwa Inu, ora lino, iwo ameneakweza manja awo, pa chikhululukiro cha machimo awo.

Page 23: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 23

Inu ndinu Mulungu, ndi Mulungu yekha. Apo pomwe iwoakhala tsopano, ndi pamene Inu mwayankhula ndi iwo. Ndipamene Inu mwawatsimikizira iwo kuti iwo ndi olakwa,pamene Mawu apeza malo Ake, ndipo MzimuWoyera unayambakuyankhula, ndi kunena, “Inu ndi olakwa. Tembenukani, ndipomubwererenso kwa Mulungu Atate.” Ndipo iwo anakwezamanja awo, kuwonetsera kuti iwo akufuna atuluke mu kholala nkhumba ili la dziko lapansi, kuti abwere ku nyumba yaAtate, kumene kuli zochuluka, kumene iwo sadzasowekerakubweretsa chirichonse. Monga mlakatuli wanena bwino,“Palibe kanthu m’manja mwanga kamene ine ndikubweretsa,mophweka basi ku mtanda wanu ine ndikukangamirako.”Mulole iwo abwere, mokoma, modzichepetsa, ndipo atsutsidwe,ndi kupereka miyoyo yawo. Ndipo Inu mudzawabweretseramwinjiro wapamwamba; ndi mphete, ndi kuika pa zala zawo;ndi kuwadyetsa iwo ndi Manna a Mwanawankhosa wophedwa.Perekani izi, Ambuye.

130 Alipo awo amene akudwala ndi otunduzidwa. Iwo ndi osowa.Satana wawaponyera iwo mu dzenje, nzosakaikitsa, akusowandalama za opareshoni. Nzosakaikitsa, mwinamwake, ambiria iwo sakanakhoza kuchitidwa opareshoni. Mwinamwakeadokotala sakanatha kuchotsa choyambitsacho, ngakhale ngatiiye akanakhala ndi ndalama zochuluka kwambiri. Koma Inundinu Mulungu. Ndipo ine ndikupemphera kuti ora lomwelino, pansi pa kudzodza kwa Mzimu Woyera komwe kuli panotsopano, kuti Inu muchiritse aliyense wa iwo. Mulole iwoachiritsidwe, kuchokera ku mutu wawo mpaka ku mapazikwawo, kachidutswa kalikonse.

131 Ngati iwo ali opanda chimwemwe; chipulumutso chawo,iwo sakukondwera nacho Icho konse. Monga Davide anati,wakaleyo, “Bwezeretsani chimwemwe cha chipulumutsochanga.” Mulole iwo alandire chimwemwe ndi chisangalalo,pa kulunda kwawo ndi kulema, pakuti Inu ndinu Thanthwemu dziko lotopetsa. Ndinu mthunzi mu nthawi ya mkuntho.Pamene mdierekezi akuvunga nthenda iliyonse ndi mzinga paiwo, Ndinu pobisalapo mu nthawi ya mkuntho. Mulole izozikhale chomwecho, lero, Mulungu, pakuti ife tikupempha izimu Dzina la Yesu. Ameni.

Mofewa ndi mwachikondi Yesu akuitana,Akuitana pa inu, ndi ine;Ngakhale ife tachimwa, Iye ali ndi chifundondi chikhululukiro,

Chikhululukiro pa iwe, ndi ine.

Bwera kwathu…

132 Tsopano ngati inu mukukhumba kutero, bwerani ku guwandipo mudzagwade pansi, ife tikhoza kupemphera nanu,

Page 24: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

24 MAWU OLANKHULIDWA

kukudzodzani inu, chirichonse chimene ife tikhoza kuchita.Ndinu olandiridwa.

…wolema, bwerani kwathu;Moona, mwachikondi, Yesu akuitana,Akuitana, O wochimwa, bwera kwathu!

133 Kodi inu mukunkonda Iye? Teddy, iwe ungatipatse ifepoyambira, “Ine ndinkonda Iye, ine ndinkonda Iye chifukwa Iyeanayamba kundikonda ine.” Kodi iwe ungapapeze?134 Tiyeni tiyimbe iyo kwa ulemelero Wake, ife tisanasinthedongosolo la msonkhano, kamphindi chabe. Uku ndikupembedza. Uthenga wapita. Ndine wokondwa kwambiri kutiinu mwaulandira Iwo. Mupemphere kuti Iwo ukuchitireni inuzabwino, pakuti iwo wandichitira ine zabwino poyankhulaIwo. Ine ndikupemphera kuti kudzodza komweko kumenekunaperekedwa kwa ine, kuti kuyankhule Iwo kwa inu,inu mwaulandira Iwo mu kudzodza komweko komwe Iwounatumizidwiramo. Ambuye adalitse Iwo ku mtima kwanu.Chabwino.

Ine ndinkonda Iye,

Tsopano ingotsekani maso anu, pamene ife tikuimba.Kwezani m’mwamba manja athu.

Ine ndinkonda IyeChifukwa Iye anayamba kundikonda ineNandigulira chipulumutso changaPa mtengo wa Kalvare.

135 Tsopano tiyeni tingoweramitsa mitu yathu, tiing’ung’uzeiyo. [M’bale Branham akuyamba kung’ung’uza Ine NdinkondaIye—Mkonzi.] Inu mukunkonda Iye? Kodi Iye siali weniwenimu mtima mwanu? Kodi palibepo chinachake chokhudza Iye,chimene chiri chenicheni basi? Ine ndinkonda Iye chifukwaIye anayamba kundikonda ine, anaponya chingwe cha Moyokuchokera kuKalvare, anadzachikoletsa icho kumtimawanga.136 Musaiwale, M’bale Kurmmond [Drummond] atilalikira ifeusikuuno, usiku wa mgonero. Ngati inu mukuwakonda Ambuye,mubwere kuno ndipo mudzadye mgonero ndi ife. Ambuyeakalola, ine ndidzakhala nanu inu kuno. Ameneyo ndi mpongoziwamwamuna wa M’bale Tonny Zabel; M’bale Thom wochokeraku Africa; mwana wake wamwamuma, mnyamata wabwino;wabwino kwenikweni, Mkhristu wokhazikika, mlaliki wabwinowamng’ono.

Chifukwa Iye anayamba kundikonda ineNandigulira chipulumutso changaPa mtengo wa Kalvare.

137 Pamene tiri ndi mitu yathu chiweramire tsopano, pamenepiyano idzipitirira.

Page 25: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO 25

138 Ambuye Yesu, ife tikukonzekera kuti tilowe msonkhanowina, Ambuye. Ife tikukuthokozani Inu chifukwa cha MzimuWoyera umene wayankhula ku mitima yathu. Ndipo ndifeokondwa, Ambuye, kuti Inu mwatichitira ife ichi. Ndipo muloleMawu Anu asabwerere kwa Inu opanda kanthu, koma muloleIwo akwaniritse icho chomwe Iwo anakonzedwa kuti adzachite.Mulole Iwo akhale mmitima yathu yonse, kudziwa kuti zinthuzonse zenizeni ndi zinthu zokhalitsa zimachokera kwaMulungu,opanda ndalama, opanda mtengo. Chifukwa chiyani ndiyeife timavutika ndi zinthu, ndi kuzipanga izo chochitika chamoyo-ndi-imfa chotero, pa zinthu zimene zidzawonongeke?Tiloreni ife tivutikire mochuluka, Ambuye, pa zinthu zimenesizidzawonongeka, zomwe ziribe mtengo. Mtengo unalipiridwakwaulere, ndi kuitana molandila, “Aliyense akufuna, Muloleniiye abwere.”139 Mudalitse gawo lotsatira la msonkhano uno. Perekaniizi, Ambuye. Ndipo mukumane nafe usikuuno. Mudalitsemsonkhanowa ubatizo. Mulole pakhale kutsanulira kwakukulu.Mulole anthu awa, amene ati abatizidwe mu Dzina la MwanaWanu wokondedwa, Ambuye Yesu, mulole iwo adzadzidwe ndiMzimuWoyera. Mulole anthu awa, amene anakweza manja awo,kuti akulapa, mmawa uno, machimo awo, mulole iwo abwere,adzalowe mu zovala za ubatizo, ndi kulowa mu dziwe, ndikudzatsimikizira kwa dziko lapansi kuti iwo akhululukidwamachimo awo. Ndipo iwo akubatizidwa, kuti iwo achotsedwemubukhu. Perekani izi, Ambuye.140 Mukhale ndi M’bale Drummond usikuuno pameneiye azitibweretsera ife uthenga, watsopano wochokera kuMpandowachifumu. Mumudzodze iye ndi MzimuWoyera. Ndipomukhale nafe pamene ife tizidya mgonero. Mulole mitimayathu ikhale yoyera ndi yangwiro, mulole pasakhale chodetsachirichonse mwa ife. Mulole Magazi a Yesu atitsuke ife kutchimo lonse. Perekani izi, Ambuye. Chotsani kudwala pakatipathu, ndipo tipatseni ife chimwemwe ndi mtendere. Kudzeramwa Yesu Khristu ife tikupempha izi. Ameni.

Ine ndinkonda…141 Kodi inu mukunkonda Iye? Tsopano kwezani m’mwambamanja anu kwa Iye.

Ine ndinkonda IyeChi-….

Tsopano fikirani ndipo mugwirane chanza ndi winawakewapafupi nanu.

…poyamba…(Russell, ine ndikunkonda Iye. Ngati ine ndingafe lero, ine

ndikunkonda Iye.)Ndipo anandigulira…

Page 26: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

26 MAWU OLANKHULIDWA

Uko nkulondola, fikirani pozungulira ndipo mugwiranechanza.

…chipulumutsoPa Kalvare…

Chabwino, M’bale Neville, ndi chonena chake.Chabwino.

Page 27: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

OPANDA NDALAMA KAPENA OPANDA MTENGO CHA59-0802(Without Money Or Without Price)

Uthenga uwu waM’bale WilliamMarrion Branham unalalikidwa mu ChingereziLamlungu mmawa, Ogasiti 2, 1959, ku Branham Tabernacle mu Jeffersonville,Indiana, U.S.A. Unatengedwa kuchokera pa matepi ojambulidwa ndi maginitonudindidwa mosachotsera mawu ena mu Chingerezi. Kumasulira uku kwaChichewa kunadindidwa mu chaka cha ndi Voice of God Recordings.

CHICHEWA

©2018 VGR, ALL RIGHTS RESERVED

VOICE OF GOD RECORDINGS, MALAWI OFFICE

P.O. BOX 51453, LIMBE, MALAWI

VOICE OF GOD RECORDINGS

P.O. BOX 950, JEFFERSONVILLE, INDIANA 47131 U.S.A.www.branham.org

Page 28: CHA59-0802 Opanda Ndalama Kapena Opanda Mtengo VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA59-0802 Without Money Or Without Price... · 4 MAWUOLANKHULIDWA ya nthawizonse. Mwinamwake, kudzakhala

Chidziwitso kwa ofuna kusindikiza

Maufulu onse ndi osungidwa. Bukhu ili mukhoza ku printa kunyumba kwanu ngati mutafuna kuti mugwiritse ntchito inuyo kapena kuti mukawapatse ena, ulere, ngati chida chofalitsira Uthenga wa Yesu Khristu. Bukhu ili simungathe kuligulitsa, kulichulukitsa kuti akhalepo ambiri, kuikidwa pa intaneti, kukaliika pakuti ena azitengapo, kumasuliridwa mu zinenero zina, kapena kugwiritsidwa ntchito ngati njira yopezera ndalama popanda chilolezo chochita kulembedwa ndi a Voice Of God Recordings®.

Ngati mukufuna kuti mumve zambiri kapena ngati mukufuna zipangizo zina zimene tiri nazo, chonde mulembere ku:

Voice of God RecoRdinGsP.o. Box 950, JeffeRsonVille, indiana 47131 U.s.a.

www.branham.org